ANATCHEZERA

Wamkulu ndine

Zikomo agogo,

Ndili ndi chibwenzi koma timasiyana ndi chaka chimodzi, wamkulu ndineyo. Kodi tingathe kukwatirana? Iyeyu akufunitsitsa atandikwatira chifukwa amandikonda kwambiri ndipo inenso ndimamukoinda zedi.

CM

Lilongwe

 

Wokondeka CM,

Zikomo pondilembera. Kusiyana zaka chisakhale chopinga kuti mukwatirane, bola chikondi ndi kulemekezana. Si chifukwa mkazi kukhala wamkulu pakubadwa bola chikondi. Chimene chimavuta nthawi zina ndi kudererana m’banja, kapena kusapatsana ulemu. Pali akazi ena amene salemekeza amuna awo ati poti iwowo ndiwo ndi aakulu pobadwa, koma pachikhalidwe chathu mkazi ayenera kulemekeza mwamuna wake ngakhale akhale wochepa msinthu ndi zaka zobadwa. Chimodzimodzi mwamuna akakhala wamkulu pobadwa naye ayenera kulemekeza banja lake, osatenga mkazi wake ngati mwana chifukwa choti ndi wa zaka zocheperako kuposa iye. M’banja laulemu mudza mwamuka akuti ‘awa ndi akazi anga’ ndipo mkazi naye amati ‘awa ndi amuna anga’ osati ‘uyu ndi mkazi wanga’ kapena ‘uyu ndi mwamuna wanga’ pagulu. Tsono ngakhale wamkulu ndiwe pobadwa umulole mwamunayo kuti mukhale thupi limodzi ngatidi pali chikondi chenicheni pakati panu.

 

Akukana woyera

Agogo,

Ndine mtsikana wa zaka 23 ndipo ndapeza mwamuna ndipo iye akuti akufuna ndimuberekere mwana koma akuti tisamange ukwati woyera. Komanso ndamva kuti anakaonetsa kale mkazi kwawo. Koma kunena zoona mwamunayu ndamukonda , nditani pamenepa?

LL,

Area 1, Lilongwe

 

Wokondeka LL,

Apa ndiye ukufuna ndikuuze chiyani, mwana wanga? Ukufunsa chinyezi m’bafa, nanga ndinene kuti chiyani? Apa zikuonekeratu kuti mwamunayu alibe chidwi choti mukwatirane koma akuti akufuna mwana, mwana wachiyani? Ungomuberekera mwana basi, mwanayo azikachita naye chiyani ngati simukhala limodzi? Iwe mwana ulibe naye ntchito? Zachibwana basi! Ndiye ukuti umamukonda mwamunayu, chikondi chako chili pati poti iye wachita kunena yekha kuti sakufuna ukwati ndi iwe koma zogonana basi, ndipo wanena wekha kuti adakaonetsa kale mkazi wina kwawo, ndiwe iwe ukufunsa kuti utani pamenepa? Umusiye basi, upeza wina wofuna banja osati zamasanje zomwe akunena mwamunayo ayi. Kulera mwana si ntchito yapafupi, imafunika banja lachikondi ndi logwirizana. Ndiye ngati iyeyo za banja ali nazo kutali ndi iwe, chotayira ntchawi yako ndi iyeyo n’chiyani?

 

A Gama abwerere

Ine ndine Mrs Jean Makolosi. Amuna anga adachoka chaka chatha kupita ku Mzuzu komwe ndamva kuti akwatira mkazi wina. Ndikufuna mwamuna wanga abwereko mwamnsanga popeza sitinayambane. Mwamuna wanga ndimamukonda, abwere mwezi uno usanathe chonde. Dzina lawo ndi a Paul makolosi Gama.

A Gama, dzimvere mtolo! Akazi anu akuti mubwerere kunyumba. Nanga banja limatha choncho? Akazi anu akuti palibe chomwe mudayambana ndipo akukukondanibe. Chonde, bwererani, ngati padali vuto anthu mumakambirana. Koma ndili ndi mawu pang’ono kwa mayi Makolosi. Amati pati bii pali munga. Zoona amuna anu adangochoka kupita ku Mzuzu kukakwatira mkazi wina popanda chifukwa? Kalipo kalipo, si wamba ayi. Chilipo chomwe chidavuta chifukwa m’banja la mtendere ndi chikondi mwamuna sangangochoka chotere n’kukakwatira kwina. Ndiye chidavuta ndi chiyani, mayi Gama? n

Share This Post