Anatchezera

ANATCHEREZA

Akundikakamira

Ndili ndi mkazi yemwe ndili naye mwana mmodzi. Vuto lake ndi limodzi: amakhalira kunyoza makolo ndi abale anga. Amati banja sakulifuna koma ndikati amange zake, amakakamira. Ndichitenji?

H,

Blantyre.

 

Zikomo H,

Kodi banja lanu mudamangitsa kuti? Kodi mudangogwiriziza kwa ankhoswe? Ngati ndi choncho bwanji osakatula nkhawazo kumeneko? Ngati mudamangitsa kumpingo, mukhonzanso kupita uko akakuthandizeni.

Banjatu sakakamiza ndipo apapa zikuonetseratu kuti mkazi wanuyo ali ndi chibwana komanso musakaike, ameneyo ali ndi wina amene amamulimbitsa mtima. N’kutheka kuti winayonso ali pabanja ndipo amamunamiza kuti adzasiya mkazi wake ndi kutengana ndi wanuyo.

Izi si nkhambakamwa, ndipo mumufufuze bwino mayendedwe ake. Samalani naye mudzalirira kuutsi atakubweretserani kwayauotche.

 

Akuti ndidzamukwatire iyeyo basi

Zikomo agogo,

Bambo ndi mayi anga adasiyana ukwati ndipo adakwatirana ndi mkazi wina yemwe analinso ndi ana ena. Mmodzi mwa anawo ndi wamkazi ndipo ndamulera mpaka kusukulu ya ukachenjede kumene akuphunzira panopa.

Vuto langa nali, iyeyo akuti sakufuna adzamve zoti ndakwatira mkazi wina chifukwa amandikonda kwambiri. Iye adati adzamuikira chiphe mkazi amene ndingadzakwatire.

Iyeyo akuti ndi bunthu ndipo akuti sadzalola mwamuna aliyense kudzamuyamba koma ine ndekha. Iyeyotu amati palibe chibale pakati pa ine ndi iyeyo. Ndichitenji?

TD,

Lilongwe.

 

TD

Monga ndanena, banja sakakamiza. Chikondi chili ngati fupa, ukakakamiza, mphika umasweka. Apatu ‘mlongo’ wanuyo ayenera kuti palibe angakakamize wina kukonda mnzake, mapeto ake ndi ngozi.

Chomwe muyenera kumuuza n’chakuti, si kuti munthu akakuchitira zabwino ndiye kuti nawenso udzikakamize kubwezera zabwino, kuphatikiza zimene zili zosadziwika bwino. Tamvapo za amayi ena amene apatsidwa mimba komanso matenda ndi abambo ena amene amawathokoza powapatsa ntchito.

Mumuuzitse kuti pamene mumamuthandiza, si kuti mumayembekezera kuti adzabwenza china chake.

Share This Post