Chichewa

Sitalaka pa Wenela

Lidali Lachinayi usiku ndipo tidali malo aja timakonda pa Wenela kukambirana izi ndi izo. Adachuluka adali madilaivala ndi makondakitala a minibasi.

Ife ojiya, osenza ndi osolola tidalipo ochepa.

“Apapa afune asafune, mawa kulibe woyendetsa minibasi kuchoka pano pa Wenela,” adayamba nkhani mmodzi mwa madalaivala.

“Komatu tikanaganiza kale. Mawalo msuzi tikaupeza kuti?” adafunsa kondakitala wina.

Koma akanadziwa! Anzakewo adamuukira, kumuthira maphuzo, monga achitira anthuwa pamsewu!

“Nkhani yavuta ndi ya msuziyo! Mabwana aja akamang’ala papolisipa kuti akatigwira tizilipira ndife osati mabwanawo. Msuzi uzikwaniranso apapa?” adafunsa wina bata litabwerera.

“Koma inuyo chikuvuta n’chiyani makamaka kuti zifike apa?” adafunsa Abiti Patuma.

“Kodi ndiwe mlendo? Apolisi ayamba kugwiritsa ntchito malamulo amene akutipweteka kwambiri. Sitikufuna zimenezo,” adatero wina.

“Kodi malamulowo ali m’mabuku?” adafunsanso Abiti Patuma.

“Kodi ukufuna kuvuta bwanji? Kapena ndi zibwenzi zako? Malamulowo ndi wokhazikika kungoti samawagwiritsa ntchito ndiye pano akufuna kutifinya,” adayankha mkulu wina, mmaso muli gwaaa!

“Komatu tinzeru tikucheperako apapa. Ndikuona kuti mutichedwetsa nazo. Tsono mukayamba kuchita zionetsero zokwiya ndi malamulo okhazikika, simukuona kuti masiku akubwerawa nawo ogwiririra adzachita zionetsero kuti chilango cha zaka 14 kwa opezeka olakwa chakula kwambiri?” adaponya funso lina Abiti Patuma.

Onse adangoti duuu!

“Ngati malamulo mukuona kuti akhwima kwambiri, mukadakambirana ndi aphungu anu kuti akasinthitse izi ku Nyumba ya Malamulo. Wina akhoza kubwerapo ndi Minibus Regulations Bill. Osati zanu za umbuli mukuchita apazi,” adapitiriza.

“Palibe, kaya wina afune kaya asafune, ife tikukachita zionetsero basi,” adatero wina, akutulutsa chikwanje.

Adachinola pamsewu.

Mawa lake ndiye kudali moto. Ndidaona anthu akuyenda wapansi kuchoka ku Ndirande mpaka m’tauni. Ochokera ku Machinjiri adali kukwera malole. Ku Manja ndi Chimwankhunda ndiye tidamva za kuphwanyidwa kwa galimoto zina. Eyi! Eyi Eyiiiiii!

Posafuna kutsalira, zigandanga za ku Machinjiri zidaotcha khoti chaka chatha zidathira moto maofesi apolisi atatu. Ati kusafuna kumangidwa.

Pomwe moto umazilala Loweruka, madalaivala aja adagwirizana zokweza mtengo wa minibasi.

Abiti Patuma adati ndimuperekeze ku Queens. Pa Mibawa, adati mtengo wakwera kuchokera pa K200 kufika pa K250.

“Chifukwa?” adafunsa.

“Kaya,” adayankha kondakitala.

Abiti Patuma adalipira K500 ya anthu awiri. Kenaka adatangwanika pa WhatsApp. Sindikudziwa ankalemba chiyani, koma uthenga womaliza udali woti: “Tikumana pachipatala pasiteji.”

Titafika pasitejipo, tidapeza kuti amalankhula ndi anzake awiri.

“Kwerani ndalipira kale kuchoka mu Blantyre ya anthu awiri. Asakulipiritseninso ameneyu. Akachita makani, manambala aapolisi aja si nkhani. Anthu ogenda kupolisi chamba chili m’thumba awa,” adatero Abiti Patuma.

Gwira bango! Upita ndi madzi!!! n

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button