Nkhani

Ankadzitama ku chipinda

Anatchereza, ine ndathedwa nzeru. Ndili pa banja ndipo ndili ndi ana atatu. Tonse timagwira ntchito. Ndisanayambe Anatche, ndiseke kaye. He he he deeee!!!!!!! Wadyapo!!!!! Amadzimva udolo!

Anthufe takhala pa banja zaka 15. Zaka zonsezi amuna anga ku nkhani ya ku chipinda ndiye adalibe mnzawo. Abambo amenewa sankatopa ayi. Masiku akalewo kaya ndikusambamo iwo zimenezo sankazimva. Chomwe amafuna ndi masewerawo basi.

Pano anasintha kwambiri ndipo ine ndakhala ndikudabwa kuti chikuchitika ndi chiyani. Kuwagwira kapena kuwakakamiza kuti tisewere, iwo amakana.

Ine pano nane ndidatopa ndikuwakakamiza. Akadzandifuna adzandiuza. Pano amuna anga apezeka ndi matenda opatsirana. Ati ali ndi chindoko, chizonono ndi ena. Kuwafunsa kuti mwawatenga kuti sakunena. Chondidabwitsa n’choti ine ndi iwowo takhala chaka tisakugonana.

Ine monga ndanenera muja kuti ndakhala ndizilakolako za iwowo koma samandithandiza. Inalipo nthawi ina yomwe amanena kuti ndituluke ku chipinda chifukwa alibe nane ntchito ndipo sakufunanso mkazi. Ndiye ngati mkazi samamufuna nanga apezeka bwanji ndi zimatenda zawozo?

Pano ndiye ndi odwalika zedi. Akuchita kulephera kuyenda.

Ndisanazindikire kuti atenga matenda ndimawadwazika, kuona ngati kuti ndimatenda enawa.

Ndidawakakamiza kuti andiuze chimwe akudwala chifukwa ndimangoona akulephera kuyenda. Atandiuza kuti akudwala zimatenda zaoozo ine zinandinyasa kwambiri. Ndimapita ku ntchito iwo akudwala ku nyumba.

Tsopano akufuna kuti ine ndiziwadwazika. Kodi ine ndikome chifukwa iwo adwala?

Anatche, ndabwera kwa inu kuti mundithandize ndisanachite chiganizo cholakwika.

Chikwawa.

Zikomo,

Ku Chikwawa kukutentha bwanji?

Mwana wanga! Akamati dziko ndi lozungulira zinthu zina zimakhala ngati zimenezi. Zoipa zomwe timapanga pansi pano, Mulungu amatilanganso pansi pompano.

Mulungu wafuna kuwaonetsa poyera kuti zomwe amachitazo ndi zoipa.

Nthawi ino asamaleni amenewo. Akapeza bwino udzawauze zonse zomwe amachitazo ndi kuwadzudzula. Dziwani kuti choipa sitibwenzera. Kumwamba Mulungu alipo oti bwenzerera. Taonanitu wakumenyelani nkhondo inu muli chete.

Komanso zones zili apo, chonde muyenera kuwauza kuti akayezetse ngati ali ndi kachirombo koyambitsa matenda a Edzi. Kuchoka apo, mukhoza kuchita chisankho choti ngati akufuna kukhala nanu limodzi ngati banja muzidziteteza. Nanunso kayezetseni!

Anatchereza

Azakhali, komwe ndimakhala ku Ndirande, kwa neba kuli mitengo ya mango yambiri. Mitengoyo nthambi zake zambiri zili kwathu. Anebawa anabwera kudzatiuza kuti mango omwe ali kwathuwa tisamathyole.

Adanena izi chifukwa anamuona mwana wathu akuthyola. Mitengo yawoyi imaipitsa pakhomo panga kwambiri. Iwo sabwera kudzasesa. Kodi ine nditawauza kuti adule nthambi zonse zomwe zilikwathu ndilakwitsa?

Ine wodandaula,

Ndirande.

Wodandaula,

Kukhala satero. Aneba anu ndi ovuta. Ngati tili ndi mitengo ya zipatso, ndipo zipatso zathu nthambi zake zili ku malo a anzathu timayenera kuwasiya kuti azidya zimenezo.

Masamba a mitengo amanyasitsa pakhomo. Oyenera kusamala kapena kusesa amakhala yemwe ali komwe kuli nthambi zimenezo. Zikatero ndiye kuti ayenera kumadya zipatsozo.

Pitani kwa aneba anuwo kuti mukakambirane nawo. Auzeni mwa ulemu kuti ngati angathe adule nthambi zomwe zili kwanuko.

Koma pa umunthu wake inu muyenera kumadya mango amenewa.

Anatchereza.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button