Nkhani

Oyendayenda achichepere Akupha msika wa amkhalakale

Amayi oyendayenda sakukondwa ndi atsikana achichepere omwe akumapezeka m’malo azisangalalo popeza akuwalanda makasitomala.

Izi zikuchititsa kuti amayiwa, amene amatchaja K10 000 nthawi yochepa ndi K20 000 usiku onse, akanike kupeza phindu popeza abambo obwera ku malo amenewa akumakonda kugonana ndi atsikana achichepere, kusiya mkhalakale.

Amodzi mwa amayi amene anadandaula za anawo. I LLoyd chitsulo

Omwe akugwira ntchito yowaunikira amayi oyendayenda mauphungu a za nkhanza komanso za ku chipatala mayi Thandiwe Kaunda ndi omwe adanena izi Lolemba.

“Atsikana achichepere amenewa akumalola kugonana ndi abambo pa mitengo yozizira monga K1 000 kapena kuchepera pamenepa. Izi zikuchititsa kuti amayi oyendayenda akuluakuluwa azisalidwa,” adatero a Kaunda.

Malingana ndi a Kaunda, izi zikuchititsa kuti amkhalakale azikanika kupeza ndalama zoti azilipira nyumba, kugula chakudya m’makomo mwawo ngakhalenso kupeza zofuna zawo za tsiku ndi tsiku.

A Kaunda adati atsikana achichepere amenewa amanama zaka zawo akafunsidwa, zomwe zimachititsa kuti akanike kuwathamangitsa m’malo azisangalalo popeza sayenera kupezekamo.

“Nanga pomwe akuluakulu amachitira zoyendayenda kuti adzithandize moyo wa tsiku ndi tsiku, ena mwa anawa amaziona zachibwana ndipo maganizidwe awo sakhala okhwima.

“Akuluakulu amaganiza za lendi, chakudya ndi zinzake,” adatero a Kaunda.

Ena mwa oyendayenda amene tinacheza nawo anati izi zikuwasokoneza kwambiri, kotero, akufuna kuti anawa achokemo m’malo azisangalalo amenewa.

Mayi wina yemwe tinacheza naye koma anapempha kuti tisamutchule dzina, anadandaula kuti kusiyana ndikale, pano amakhala usiku onse osapeza kanthu.

Iwo adati: “Abambo akumatisiya chifukwa anawa akumatchipitsa. Choncho, saganiza zoti angatitengenso.”

Amayiwa anati kupezeka kwa anawa m’malo achisangalalo amenewa kwapangitsa kuti moyo wawo ulimbe koopsa.

“Penanso eni a malo amenewa amasangalala akakhala kuti anawa abwera chifukwa amadziwa kuti anthu agula mowa kwambiri chifukwa abambo okonda anawa achulukirapo,” iwo adatero.

Kafukufuku wathu akusonyeza kuti ambiri mwa ana oyendayenda amenewa amakhala kuti adali opemphetsa m’misweu ndiye akula ndi kuyamba mchitidwewu.

Enanso mwa anawa amachita kutumidwa ndi makolo kapena omwe amawasunga.

Koma wachiwiri kwa mneneri wa polisi a Harry Namwazi Lachinayi adati anawa amachotsedwa m’malo a zisangalalo akapezeka.

“Koma mu zonse, si ntchito ya apolisi okha kuthana ndi zimenezi. Anthu akuyenera kudziwitsa apolisi kuti tikwanitse kumanga omwe akugona ndi anawa ngakhaleso akulimbikitsa anawa kupezeka akupanga zoyendayenda,” adatero iwo.

Malingana ndi gawo 146 la malamulo a dziko la Malawi, amayi oyendayenda ndi otetezedwa ku zinthu zosakhala bwino monga nkhanza.

Poyankhula ndi Msangalutso Lachiwiri, mmodzi mwa akulu akulu ku bungwe la Centre for Human Rights Education Advice and Assistance mayi Ruth Kaima, anati malingana ndi malamulo, kugonana ndi anawa ndi mlandu.

“Malamulo amati kugona ndi mwana ndi mlandu ngakhale atapezeka pa msewu kapena ku malo achisangalalo ndipo mwagwirizana,” a Kaima anatero.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button