Nkhani

Anthu 537 akusowabe chichitikileni namondwe

Listen to this article

Nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya DoDMA yati tsopano apolisi angolengeza kuti anthu 537 omwe akusowabe chichitikireni namondwe wa Freddy adamwalira.

Mkulu wabungwe la DoDMA a Charles Kalenba ati sabata zitatu zofufuza anthuwo zachuluka moti n’zokaikitsa kuti angakhale ndi moyo mpaka pano pomwe ena 676 adatsimikizika kale kuti adamwalira.

“Pofika Lolemba lapitali, anthu 537 adali asadapezekebe ndipo magulu ena akadayang’ana anthuwo. Pamudzi wa Ntauchila m’boma la Chiradzulu mudzi onse udapita ndipo apolisi ayesetsa kuyang’ana anthuwo ndi agalu komanso magulu ena koma palibe chomwe apezako moti tangotseka ntchito yoyang’anayo,” adatero a Kalenba.

Iwo adati namondweyo adavulaza anthu 2 171, anthu ena 659 278 akusowa pokhala ndipo akusungidwa mmisasa 747 yomwe idakhazikitsidwa mmalo osiyanasiyana.

“Nyumba za mabanja 882 989 zidagumuka moti anthuwo ndiwo akusungidwa m’misasa,” adatero a Kalemba.

Malingana ndi nthambi ya DoDMA, anthu pafupifupi 2.3 miliyoni m’maboma 13 mbewu ndi ziweto zawo zidakokoloka ndipo zipatala zing’onozing’ono 63 zidakokoloka.

Boma la Blantyre ndilo lili ndi anthu ambiri okhudzidwa okwana 434 586 motsatana ndi Mulanje yomwe ili ndi anthu 362 135. Zomba ili ndi anthu okhudzidwa 322 938, Phalombe 258 557, Mangochi 230 373 ndipo Chiradzulu anthu 191 883.

Omwe akutsogolera gulu la asilikali a nkhondo omwe akuyang’ana anthu osowawo a Major General Saiford Kalisha adauza atolankhani kuti asilikali 140 akadayang’ana anthu omwe akusowawo.

Iwo adaonjeza kuti asilikali ena 179 odziwa zomangamanga ochokera ku Malawi ndi Tanzania akugwira limodzi ntchito yomanga misewu ndi milatho kuti anthu oyang’ana anthu osowa ndi opereka thandizo losiyanasiyana asamavutike kufika m’madera.

DC wa boma la Mulanje a David Maxwell Gondwe komanso a Douglas Moffat aku Phalombe adati m’mabomamo mukadali mavuto adzaoneni.

Mwa thandizo lomwe labwera kwa okhudzidwa, dziko la Zimbabwe lapereka matani 300 achimanga ndipo kazembe wadzikolo a Nancy Saungweme adati maiko a Malawi ndi Zimbabwe ndi apawo n’chifukwa chake amathandizana m’zambiri.

“Zikakugwerani Ife tikuyenera kukukutani, ndiponso timayenera kukhala woyambilira kubwera ndi thandizo chifukwa tili m’khonde ndipo timayenera kuthandizana,” adatero a Saungweme.

Koma a Kalemba adadzudzula andale ena omwe apezerapo danga pathandizo lomwe ena akupereka kuti lithandize anthu omwe adakhudzidwa ndi namondwe wa Freddy.

Related Articles

Check Also
Close
Back to top button