Nkhani

Lamulo la za ngozi zadzidzidzi lanunkhira

Lamulo lounika za ngozi zogwa mwadzidzidzi latsala pang’ono kupsa malingana ndi zomwe mkulu woyang’anira zopanga malamulo ku unduna wa za malamulo a Amam Mussa anena.

Mwa zina, lamulo latsopanolo lidzakonza ndondomeko yokonzekera bwino ngozi za dzidzidzi mmalo mongokamba zoyenera kuchita ngozizo zikachitika.

Katundu wambiri adakokoloka ndi namondwe wotchedwa Freddy

A Mussa amapereka tsatanetsatane wa momwe ntchito yophika lamulolo ikuyendera ku komiti yoona za za chilengedwe ndi kusintha kwa nyengo.

“Tikupanga zotheka kuti Bilu ya lamulolo ipite ku Nyumba ya Malamulo mkumano omwe uli mkatiwu potsatira zomwe adalonjeza a Pulezidenti a Lazarus Chakwera kuti lamulolo litheka,” adatero a Mussa.

Komitiyo komanso mabungwe achilimika kufuna lamulolo litakhazikitsidwa potsatira ngozi ya Namondwe wa Freddy yemwe adaononga m’maboma a m’chigawo cha kummwera.

Wachiwiri kwa mkulu woyang’anira za ngozi zogwa mwadzidzidzi a Fyaupie Mwafongo ati lamulo lomwe likugwira ntchito pano ndilopelewera muzina chifukwa limangokamba zoyenera kutsatidwa ngozi ikagwa.

“Tikufuna lamulo lomwe lizifotokoza ndondomeko yoyenera kutsata popewa ngozizo zisadagwe nkomwe. Timaononga ndalama zochuluka ngozi zikagwa koma titha kuchepetsa ndalamazo popewa ngozizo zisadagwe,” atero a Mwafongo.

Iwo ati lamulo latsopanolo lizidzapereka mphamvu ku boma zoti litha kuthamangitsa anthu m’madera momwe likuona kuti mutha kugwa ngozi ndipo likhoza kupereka chilango kwa anthu ozengereza.

M’madera ambiri a m’dziko muno anthu adamanga m’mapiri ndi m’mitsinje koma a Mwafongo ati kumakhala kovuta kuwasuntha m’malomo chifukwa palibe lamulo lomwe limatsindika za komwe anthu angamange n’kukhazikika.

“Mchitidwe umenewu wameta mapiri nchifukwa chake madzi ankati aphulike akumabwera ndi mphamvu nkumaononga choncho lamulo lomwe likubwera lidzidzaunikira zonsezi,” atero a Mwafongo.

Woyendetsa mapulogalamu ku bungwe lomangira anthu nyumba la Habitat for Humanity  a Lucy Mwale ati mchitidwe wolekelera anthu kumanga mmalo osayenera ukuwonjezera umphawi wa nyumba.

Iwo ati anthu 75 mwa anthu 100 aliwonse amakhala mnyumba zosalongosoka ndipo izi zimayika miyoyo ndi katundu wawo pachiwopsezo.

“Panopa timayenera kuti tizimanga nyumba 25 000 chaka chilichonse kwa zaka 10 kuti mavuto anyumba achepe ndiye mukawona sintchito yamasewera ayi chifukwa pakufunika ndalama zambiri,” atero a Mwale.

Wapampando wa mgwirizano wamabungwe owona zachilengedwe ndikusintha kwa nyengo a Julias Ng’oma ati Bilu yomwe ikubwerayi ikadabwera kalekale, ngozi zina zomwe zagwa mdziko muno pakatipa sizikadawononga ngati momwe zidachitira.

“Lamulolo linkayenera kukhala litapsa mchaka cha 2017 ndipo bwenzi latithandiza kupewa ngozi zina zomwe zidatigwera. Lamulolo likuyembekeza kudzasintha momwe timachitira zinthu zina zokhudza chilengedwe,” atero a Ng’oma.

Wachiwiri kwa wapampando wa komiti yowona za zachilengedwe ndikusintha kwa nyengo a George Katunga Miliyoni adati Nyumba ya Malamulo ikungodikira biluyo kuti akayipange kukhala lamulo.

“Panopa dziko lonse lili nchiyembekezo chachikulu mu Bilu imeneyi ndiye tikungodikira kuti itipeze kunyumba ya Malamuloyo atikayipange kukhala lamulo,” atero a Miliyoni.

Iwo ati omwe akupanga lamulolo akuyenera kuchita machawi kuti aphungu akamadzatseka mkumano wa bajeti ya 2023/2024, biluyo idzakhala itadutsa ku Nyumbayo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button