Nkhani

Anthu aphunzitsidwe zauindo wawo—Nice

Listen to this article

Bungwe la National Initiative for Civic Education (Nice) Public Trust lati dziko lino likulephera kutukuka chifukwa choti anthu ambiri sadaphunzitsidwe za ufulu komanso udindo wawo pa zinthu zosiyanasiyana, kuphatikizapo ntchito za chitukuko.

Mkulu wa Nice Trust, Ollen Mwalubunju, ndi yemwe adanena izi Lolemba potsegulira maphunziro a masiku atatu a ogwira ntchito zophunzitsa anthu kubungweli.

Maphunzirowa adachitikira m’boma la Blantyre ndi thandizo lochokera ku bungwe la mgwirizano wa maiko a ku Ulaya la European Union (EU).

Mwalubunju adatsindika kuti, kwa zaka zingapo, boma lakhala likugwira ntchito zachitukuko popanda kupereka mpata kwa nzika kuti zitengepo gawo pa ntchitozo.

“Choncho, mpofunika kuti boma komanso mabungwe ngati ife a Nice Trust lichilimike pophunzitsa anthu za maufulu omwe ali nawo komanso ndi udindo womwe ayenera kusenza kuti chitukukocho chitheke,” iye adatero.

Mwalubunju adapempha ogwira ntchito zophunzitsa anthu m’maboma kuti akhale patsogolo pa ntchitoyi.

“Ife a Nice Trust tili ndi kuthekera konse pantchitoyi potengera ntchito yomwe takhala tikugwira pophunzitsa anthu zachisankho mmbuyomu,” adaonjeza.

Mkuluyo adathokoza bungwe la EU kaamba ka thandizo lomwe lidapereka kuti Nice Trust igwirire ntchito zake zophunzitsa anthu kwa zaka zingapo.

Related Articles

Back to top button
Translate »