Nkhani

Aphungu akumana

Listen to this article

Mkumano wa aphungu aku Nyumba ya Malamulo ulimkati ku Lilongwe ndipo mtsogoleri wanyumbayo a Richard Chimwendo Banda ati nkhawa zikuluzikulu za Amalawi zili pa mndandanda wa zokambirana.

Zina mwa nkhawazo malingana ndi maganizo a mafumu omwe adalankhula ndi Tamvani sabata zapitazo ndi kusowa kwa mafuta a galimoto, nkhani ya njala, kuvuta kwa magetsi, kusowa kwa ndalama zakunja ndi kukwera kwa mitengo ya zinthu.

Patangotha sabata imodzi Tamvani itasindikiza za nkhawa za Amalawiwo kudzera mwa mafumu akuluakulu, mtengo wachimanga udakwera kufika pa K25 000 pa nthumba la makilogalamu 50 mmadera ena.

Malingana ndi mkulu wa bungwe lowona za anthu ogula katundu la Consumers Association of Malawi (Cama), izi zikuchitika pomwe tikulowera mmiyezi yomwe njala imavuta kwambiri ya November mpaka March ndipo malipoti akusonyeza kuti anthu pafupifupi 3.8 miliyoni alibe chakudya.

Akapito ati mmalo motaya nthawi ndimikangano yopanda pake, aphungu akuyenera kumenya nkhondo yoti msika wa Admarc utsegulidwe kuti mwina mtengo wa chimanga ungagweko.

“Kutseka kwa Admarc kudapangitsa kuti msika wa chimanga ukhale m’manja mwa mavenda n’chifukwa chake mitengo ikungokwera mosadziwika bwino chifukwa Admarc ikatsegulidwa, imakhala ngati ikumanga mitengo,” atero a Kapito.

Iwo ati boma lidakhazikitsa malipiro oyambirapo pa K50 000 kutanthauza kuti ngati mtengo wachimanga uli K25 000 ndiye kuti munthu akhoza kungogula matumba awiri pamalipiro a mwezi wonse nkusiya mavuto ena akungobelekana.

Koma a Chimwendo Banda apereka chiyembekezo choti mwina mayankho a nkhawa ngati zimenezi n’kupezeka chifukwa aphungu azikambirana malingana ndi mndandanda wa zokambirana zawo.

“Nkhawa zimenezo zili pamndandanda wazokambirana kuphatikizapo zokhudza malamulo oyendetsera zisankho ndi oweruzira mirandu,” adatero a Chimwendo Banda.

Mkumanowo ndi wounika momwe bajeti ya 2022-2023 ikuyendera polingaliranso kuti ndalama ya Kwacha idagwa ndi K25 bajetiyo itadutsa kale ku Nyumba ya Malamulo.

Mkulu wabungwe loona zoti zinthu zikuchitika poyera la Centre for Social Accountability and Transparency a Willie Kambwandira ati akuyembekezera kuti bajetiyo isinthidwa mwina ndi mwina kuti zigwirizane n’kugwa kwa ndalamayo.

“Zimenezi zikukhudza kuunikira madera monga okhudza kusowa kwa mafuta, gwedegwede wa pulogalamu ya AIP ndi mavuto ena omwe akula mdziko muno,” atero a Kambwandira.

Iwo ati ngati aphunguwo amalingalira za anthu omwe amawayimilira, akuyenera kupachika kusiyana kwawo pa ndale nkuyika mtima popeza mayankho amavuto a Amalawi.

Kadaulo pa zachuma a Betchani Tchereni ati nkofunikiradi kuti pounika bajetiyo, aphunguwo aganizire nthambi zofunikira kwambiri pachitukuko cha dziko kuti mavuto omwe alipo apepuke.

Mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma m’nyumbayo a Kondwani Nankhumwa ati kupatula kukambirana nkhawa zomwe Amalawi apereka, aphungu akufuna nduna ya zachuma a Sosten Gwengwe apereke tsatanetsatane womveka bwino wa momwe boma layendetsera bajeti m’miyezi yaitayi.

A Nankhumwa anena izi polingalira malipoti woti mkatikati mwa bajetiyo mwachitika zachinyengo zosiyanasiyana zoyenera kuunikidwa kuti Amalawi akhale n’chikhulupiliro pa Nyumba ya Malamulo.

“Mwa zina, tikufunanso anduna a zachuma atafotokoza bwino ndondomeko zomwe boma lakonza pofuna kudzutsa chuma cha dziko lino,” atero a Nankhumwa.

A Gwengwe akuyembekezeka kudzapereka lipoti la momwe chuma chayendera m’miyezi yapitayo Lachisanu likubwerali ndipo akadzatero, aphungu adzayamba mtsutso pa zomwe a Gwengwewo adzanene.

Related Articles

Check Also
Close
Back to top button