Banda adataya mwayi
Mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda adataya mwayi wosonyeza bwino lomwe kuti akudziwa chimene akuchita polimbana ndi chiwanda chidalowa kulikulu la dziko lino kumene ogwira ntchito m’boma agundika kupakula ndalama.
Mmalo monena zimene akuchita, iye adataya nthawi yaitali kunena kuti kubako kudayamba zaka 20 zapitazo. Atolankhani ena atamufunsanso ngati achotse nduna ya zachuma, oyendetsa chuma cha boma komanso mlembi wamkulu mu ofesi ya pulezidenti ndi nduna zake, iye adati sangatero.
M’mbuyomu, Banda adaneneratu kuti adadziwa za kupakula kumene kumachitikako miyezi isanu yapitayo. Tsono tikudabwa kuti atazindikira adachitapo chiyani? Nanga n’chifukwa chiyani palibe chimene amachita kufikira mkulu woyendetsa ndondomeko ya zachuma Paul Mphwiyo adaomberedwa?
Kunena kuti sangachotse ntchito akuluakuluwo kukusonyeza kuti pali china chimene if sitikuuzidwa. Khoswe wakhala pa mkhate apa. Akuluakuluwo amayenera kutula pansi maudindo awo okha, osadikira kuchotsedwa izi zitaphulika. Chifukwa choti sadachite izi, ambiri amayembekeza awachotsa.
Kuchotsa akuluakuluwo ndi njira imodzi yoti kufufuza kuyende bwino.
Ndalama zimene zimaseweretsedwazo si za Banda kapena akuluakulu a bomawo ayi. Izi ndi ndalama zimene Amalawi amakhetsera thukuta pokhoma misonkho. Izi ndi ndalama zimene zikakadathandiza Amalawi pachitukuko: kumanga sukulu, zipatala, kutukula ulimi ndi ntchito zina zotere.