Nkhani

 Chiyembekezo chakwera ndi mawu a Chakwera

Listen to this article

Pakati pa usiku wa Lachitatu sabata yatha, ndalama ya kwacha idatsika mphamvu ndi K44 pa K100 iliyonse. Izi zachititsa kuti mitengo ya katundu ikwere, zimene zikufinya Amalawi.

Amalawi akhala akupereka nkhawa ndi kugwa kwa Kwacha komanso kukwera kwa mtengo wakatundu makamaka fetereza panyengo ino pomwe dziko likulowa nyengo ya dzinja.

A Chakwera: Nduna zili kunja zibwereko

Ena mwa Amalawi omwe amalankhula poyera za nkhawa zawo amadzudzula a Pulezidenti a Lazarus Chakwera kuti akuyendayenda kwambiri zomwe iwo amati zikutha ndalama zakunja zomwe bwenzi boma likugulira katundu yemwe amachokera kunja monga feterezayo.

Koma polankhula ku mtundu wa Amalawi atachoka kunja usiku Lachitatu, a Chakwera adatambasula mfundo zotupitsira ndalama za boma zomwe adalonjeza kuti zigwira ntchito yogula fetereza ndi chakudya kuti anthu asakhale ndi njala.

“Ndalama zomwe tipulumutse pandondomeko yomwe takonza tiyigwiritsa ntchito pogula fetereza ndi chakudya kuti anthu paliponse m’dziko muno akhale ndi chakudya chokwanira,” adatero a Chakwera.

Mwa mfundo zina zopulumutsira ndalamazo, a Chakwera ati adula maulendo awo onse kuyambira ulendo omwe adali nawo kumapeto a mwezi uno wokakambirana zokhudza kusintha kwa nyengo.

Iwo adatinso akuluakulu a boma aziyenda pogwiritsa ntchito ndalama zaboma pokhapokha iwo akauzidwa zifukwa zaulendowo ndipo akaona kuti ngofunika kwambiri azipeleka okha chilolezo.

“Pachifukwachi, nduna zonse komanso akuluakulu ena aboma omwe adapita kale kunja pa ndalama zaboma akuyenera kubwerako pompano,” adatero a Chakwera.

Iwo adalamulanso kuti nduna zonse ndi akuluakulu ena a m’boma omwe amalandira mafuta a galimoto tsopano azingolandira theka la mafuta omwe amalandira.

Poyankha nkhawa yoti zinthu zakwera mwadzidzidzi anthu asadakonzekere komanso ndalama zomwe amalandira zikadali zochepa, a Chakwera adati alamula nduna yazachuma a Simplex Chithyola Banda kuti awunike zinthu zingapo.

“Ndauza nduna ya zachuma kuti pomwe kuunika bajeti kuli mkati, ayikemo gawo lothandizira a bizinesi zing’onozing’ono, awunike malipiro a ogwira ntchito m’boma komanso misonkho womwe anthu amapeleka kuchoka kumalipiro awo,” adatero a.Chakwera.

Iwo amalankhula zonsezi patangotha ola limodzi akuluakulu International Monetary Fund (IMF) atalengeza kuti tsopano dziko la Malawi likhoza kuyambiranso kulandira thandizo lake.

Potsatira izi, a Chakwera adati maiko ndi mabungwe osiyanasiyana omwe adasiya kuthandiza pa bajeti ya Malawi ayamba kulonjeza kuti ayambiranso kuthandizapo.

Papita zaka pafupifupi 10 maikowo chisiireni kuthandiza Malawi kaamba ka momwe maboma apitawo ankayendetsera  nkhani zachuma ndipo IMF idaimitsa thandizo ku Malawi mu 2020 chifukwa boma lapitalo lidapereka malipoti abodza kubungwelo.

Koma a Chakwera adati athana ndi akuluakulu onse omwe adatengapo gawo lililonse kuti dziko la Malawi likapezeke mmavuto azachuma omwe adathamangitsitsa olithandiza.

Izi zidayankha mafunso ena omwe kadaulo pa zachuma a Christopher Mbukwa adatambasulira Tamvani mmawa wa Lachitatu a Chakwera a k u y e m b e k e z e k a kulankhula madzulo ake.

“Pomwe zinthu zafika, a Pulezidenti akuyenera kupereka chilimbikitso pa nkhani yokwenza malipiro, kuthandiza abizinesi zing’onozing’ono kuphatikizapo alimi ang’onoang’ono.

“Mwachidule akuyenera k u p a t s a A m a l a w i chiyembekezo choti kugwa kwa Kwacha simathero koma kuti atero atambasule bwinobwino zomwe apange kuti zitheka,” adatero a Mbukwa.

Koma a Chakwera atamaliza kulankhula, a Mbukwa a d a u z a nyuzipepala ya.The Nation kuti a Pulezidenti adayankha nkhani zofunika muuthenga wawo.

Mmawa wa Lachitatu lomweri, mfumu yayikulu Mwankhunikira ya ku Rumphi idati anthu ali ndi nkhawa yaikulu makamaka pa nkhani ya fetereza yemwe tsopano adafika pa K107 000 boma litachepetsanso chiwerengero chaopindula mu AIP.

“Apapa akonzepo chifukwa ngakhale mu AIP mavuto ayamba kale, anthu omwe amakagula fetereza wa AIP ku Mhuju kuno ku Rumphi abwerera akuti netiweki pomwe ena maina asokonekela,” adatero a Mwankhunikira.

Koma pa zakufewa kwa IMF, mkulu wabungwe la akadaulo pa zachuma la Economics Association of Malawi (ECAM) a Betchani Tcheleni adati mpofunika kusamala kwambiri kuti thandizo ngati limeneli lisadzathawenso.

Mwa z i n a , iwo a d a t i m p o f u n i k a kutsatira ndondomeko zopulumutsira ndalama makamaka zakunja podula maulendo ena omwe siwofunikira kwambiri komanso kuonetsetsa kuti pomwe ndalama zikhoza kupulumutsidwa, mpata wotero ukugwira ntchito.

M g w i r i z a n o w a mabungwe omenyera ufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) nalo latulutsa kalata yake yoyamikira ndondomeko zomwe a Chakwera adatambasula.

“ N d o n d o m e k o zimenezija nzopeleka chiyembekezo kwa Amalawi koma poti nthawi zina chimavuta nkukwaniritsa, a Pulezidenti akhazilitse komishoni ya kalondolondo pa zomwe anena,” yatero HRDC mkalata yake.

Ilo lidachenjeza boma Kwacha itangogwa mphamvu kuti likuyenera kupeza njira zoti kugwa kwa Kwacha kusabweretse ululu waukulu kwa anthu.

Related Articles

Back to top button
Translate »