Chichewa

Kamatira: Nthenda yosautsa

Listen to this article

 

Thenda zina ukazimva mmakutu kuchita kuwawa chifukwa chakuwopsa kwake. Anthu ambiri amataya mtima ndi matenda aja a Edzi komatu kunjaku kulinso matenda ena omvetsa ululu wadzawoneni. Ena mwa matenda otere ndi aja ena amawatcha kamatira. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Socrates Mbewe zokhudza matendawa ndipo machezawo adali motere:

A Mbewe, tandifotokozerani kuti mumachokera kuti ndipo mumatani.

Choyamba ine kwathu ndi ku Sawawa kwa mfumu yaikulu Chikowi ku Zomba. Pano ndili muno mu mzinda wa Lilongwe kuthandiza anthu makamaka pankhani ya mankhwala azitsamba. Mwachidule ndine sing’anga.

Mbewe: Ndachiritsa ambiri odwala kamatira
Mbewe: Ndachiritsa ambiri odwala kamatira

Ndimangomva za matenda a kamatira, kodi amenewa ndi matenda anji?

Malume, amenewa ndi matenda osautsa kwabasi. Munthu amangomva mseru, kubaya ndi kupotokola m’mimba koma kuti achite chimbudzi kapenanso kutaya madzi amalephera ndiye amakhala akumva ululu koopsa.

 

Kwenikweni matenda amenewa amayamba bwanji?

Pali njira zosiyanasiyana. Zina zachilengedwe zomwe angafotokoze bwino ndi achipatala komanso pali njira za mwa anthu zochita kuponyerana zomwe kuthana nazo kwake ndi kuchikuda basi.

 

Kuwazindikira kwake akamayamba ungawazindikire bwanji?

Ndilankhula kwambiri kumbali yachikudayi chifukwa ndiko ndimadziwa kwambiri monga ndanena kale. Matenda amenewa ali mitundu pawiri. Pali kamatira wamoto yemwe munthu amangomva kutentha m’mimba ndi m’chikhodzodzo koma kumalephera kudzithandiza ndipo ngati sadathandizidwe, masiku 7 ndi ambiri akhoza kupita. Mtundu wina ndi wa kamatira wozizira yemwe munthu amatha kukhala sabata zitatu akungomva ululu.

 

Inuyo mudathandizako munthu wa vuto limeneli?

Ambirimbiri ndipo amabweranso okha kudzandithokoza chifukwa cha chikumbumtima cha ululu chomwe amakhala nacho. Ndathandiza anthu ambiri m’madera osiyanasiyana osati kuno kokhanso, ayi.

 

Mankhwala ake mumatani?

Pali zizimba zake. Koma chachikulu nchakuti timasema mtengo wa mankhwalawo n’kuusakaniza bwinobwino ndiye munthu uja amathira theka la supuni yaing’ono muphala n’kumwa. Akatero amatsegula m’mimba kwambiri ndipo zotulukazo zimakhala zakuda kwambiri ngati makala okanyakanya.

 

Komano oponyerayo amachita bwanji?

Pali njira zosiyanasiyana koma machitidwe ake ndi amodzi. Ena amatapa chimbudzi kapena mkodzo olo madindo amatako. Ena amagwiritsa ntchito nsima yotsala kwa munthu yemwe akufuna kulodzayo kapena nkhoko zam’poto momwe mudaphikidwa nsimayo. Machitidwe ake, amatenga zomwe ndatchulazi n’kusakaniza ndi mankhwala kenako n’kuika muchithu chosachucha kapena kudontha. Ambiri amakonda bango ndipo mkatimo amasakanizamo singano kuwonjezera ululu uja.

 

Ndiye kuchira kwake ndi kwa asing’anga basi?

palibenso njira ina ngati zili zoponyeredwa, apo bii ndiye kuti wolodzayo akhululuke n’kumumasula mnzakeyo. Zikakhala zachilengedwe ndiye mapilitsi aliko kuchipatala, munthu amatha kumwa n’kutsekula m’mimba bwinobwino. Koma chachikulu choti mudziwe n’chakuti si onse omwe amadziwa mankhwala ake, ena sadziwa koma amangokakamira chifukwa

chofuna makobidi. Sing’anga weniweni akaunika, ngati zili zachilengedwe amamuuza chilungamo munthu.

 

Koma muzonse zomwe mwakumana nazo inuyo mumapeza kuti chimachititsa anthu kuponyerana nthenda yoopsayi n’chiyani?

Nkani yaikulu imakhala dumbo. Ngati munthu wina amachita nawe nsanje ndiye akuganiza njira yokuzunzira kapena ngati anthu adayambana ndiye winayo akufuna kumvetsa mnzakeyo kuwawa mpamene izi zimachitika.

 

Amati matenda ena oponyerana amatha kuwabweza kwa woponyayo, awanso zingatheke?

N’zotheka ndipo awa okha ndi ngozi chifukwa ukamponyera mnzako iye n’kupondaponda n’kukubwezera, iweyo suchiranso mpaka ulendo pokhapokha yemwe udamuponyerayo adzazonde matenda ako koma ambiri amavuta kukazonda matenda a munthu yemwe akudziwa kuti adawaponyera zowawa ngati kamatira.n

Related Articles

Back to top button
Translate »