Kudali ku msonkhano wa mapemphero
Mbusa Willard Maluwa yemwe akutsogolera mpingo wa Fountain of Victory m’boma la Salima adakumana koyamba ndi mkazi wake Abgail Mkwate yemwe amagwira ntchito ku kampani ya TNM ku msonkhano wa mapemphero womwe udachitikira m’boma la Ntcheu m’chaka cha 2016.
“Nditangomuona mtima wanga udapeza mtendere koma sikuti ndidatengapo sitepe yomufunsira ayi koma tidayamba kucheza,” adatero Maluwa.
Awiriwo adakhala pa chinzake kuchokera chaka cha 2016 kufika 2018 ndipo m’chaka cha 2018 ndi pamene Maluwa adafunsira, koma sadamulole pompopompo.
“Mkazi wanga adayamba kukafunsira nzeru kwa akuluakulu monga Mama Apostle Joseph Ziba ngati kudali koyenera kuyamba ubwenziwo pokonzekera ukwati,” adatero mbusayu.
Apatu ubwenzi wawo udayamba ndipo pofika pa September 7 2019 adadalitsa ukwati wawo pa mpingo wa Fountain of Victory, madyerero adachitikira ku Chrichi Gardens ku Chitawira mu mzinda wa Blantyre.
Awiriwo akulangiza achinyamata omwe ali pa chibwenzi kuti alole mantha a umulungu k awaphunzitse m’mene angayendetsere chibwenzi chawo.
Iwo akuti Mulungu ndiye mwini banja. Choncho akuyenera kumutsogoza pa china chilichonse kuti cholinga chake pa banjalo chikwaniritsidwe.
“Tikakumana ndi vuto m’banja mwathu, timafunsira nzeru kwa Apostle Ziba ndipo amatithandiza,” adatero Mkwate.
Pamene Maluwa amachokera m’mudzi mwa Undani, Mfumu Kapeni m’boma la Blantyre, Mkwate amachokera m’mudzi mwa Mjojo, Mfumu Mlumbe m’boma la Zomba.
Pakadali pano awiriwo akukhalira pa boma ku Salima komwe akutumikira pa mpingo wa Fountain of Victory ndipo Mkwate tsopano ndi mayi busa Maluwa.