Akufuna mwana
Gogo,
Ndakhala m’banja ndi mwamuna wanga zaka zisanu, koma wopanda mwana.
Mwamuna wanga amalimbitsa mtima kuti ndisadandaule popeza mwana ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, koma abale ake ndi anga sakuimva. Akundivutitsa akuti akufuna mwana.
Nthawi zina akwawo amabwera kudzandiuza kuti ndichoke pakhomopo chifukwa ndilibe phindu.
Nditani?
HGP
HGP,
Ndiyamike mwamuna wanu kaamba koti ndi munthu wokoma mtima, komanso wachikondi.
Akadakhala amuna ena akadakuvutitsani.
Ndigwirizane ndi mwamuna wanu kuti mwana ndi mphatso ndipo Mulungu amapereka mu nthawi yake osati yathu. Choncho abale a mwamuna wanu ndi abale anu akulakwa kumavutitsani.
Nanga akudziwa bwanji kuti vuto ndinu?
Ndikufuna ndikupempheni kuchita zinthu zitatu. Choyamba, pitani ku chipatala mukawafotokozere vuto lanu.
Chachiwiri, limbani mtima. M’moyo wathu timakumana ndi mavuto osiyanasiyana, koma timayenera kulimba mtima.
Chachitatu, mufunseni Ambuye kuti alowerere pa vuto lanu.
Natchereza
Akundikana
Gogo,
Ndakhala ndikumufunsira mtsikana wina kwa zaka zitatu tsopano, koma amangondiyankha pompopompo kuti sakundifuna.
Poyamba ndimaona ngati ndimomwe atsikana amachitira mnyamata akawafunsira, koma panopa ndayamba kuda nkhwawa.
Nditani?
BNM
BNM,
Fupa lokakamiza silichedwa kuswa mphika.
Ngati mtsikanayo akukukanani kuti sakukufunani musamukakamize. Musiyeni.
Mwina mukadakhala ndi chiyembekezo akadakuuzani kuti mumudikire aganize kale, koma kukuyankhani pompopompo kuti sakufuna sikukupereka chiyembekezo chilichonse.
Musadandaule, mudzapeza mtsikana wina wokukondani.
Natchereza
Akuchita nsanje
Gogo,
Mtsikana wina ndinamufunsira ndipo anandikana, koma nditapeza mnzake adandilembera kalata yokhumudwa.
Adandiuza kuti ndimusiye mtsikana winayo ndipange chibwenzi ndi iyeyo.
Ndithandizeni.
DPK
DPK,
Musalole. Adakukanani ndipo inu mudalimba mtima ndi kupeza mnzake. Nanga akufunanso chiyani?
Musalole kulakwira mtsikana winayo poonetsa kukhulupirika kwa mtsikana amene adakukanani kale ubwenzi.
Natchereza
Ndikufuna mkazi
Gogo,
Ndine mnyamata wa zaka 26 ndipo ndikufuna mkazi woti ndimange naye banja.
Mkaziyu akhale woti sanaberekepo, komanso wa zaka zosaposa 25.
Ine ndikukhala ku Area 25 mu mzinda wa Lilongwe ndipo amene ali wokonzeka kulowa m’banja ayimbe 0990 920 810.
PPK,
Lilongwe