Chichewa

‘Kudali ku Presbyterian Church of Malawi’

Listen to this article

Kudali kuphwanya mafupa ku Dream Centre Assemblies of God mumzinda wa Blantyre Loweruka pa 2 May pamene Faith Mussa amachititsa ukwati ndi bwenzi lake Brenda Chitika.

Ndi kanamwali kopanda banga, kopanda chipsera. Thupi losalala komanso kathupi lomva mafuta.

Ikokatu ndi ka m’mudzi mwa Sikoya kwa T/A Chikumbu m’boma la Mulanje. Iko ndi kachinayi kubadwa m’banja la ana asanu.

Faith Mussa kuimbira namwali wake kanyimbo kachikondi
Faith Mussa kuimbira namwali wake kanyimbo kachikondi

Faith amene adatchuka kwambiri ndi nyimbo ya Desperate, akuti ubongo wake udasokonekera pamene adaona njoleyi Lamulungu mu 2009 pomwe mnyamatayu adapita kumpingo wa Brenda wa Presbyterian Church of Malawi (PCM) mumzinda wa Blantyre kukatsitsimuka.

Faith adatsitsimuka zenizeni chifukwa kusalalanso kwa njoleyi kudaziziritsa mtima wake. Tsikuli Mulungu adakumana ndi chosowa chakedi.

“Ndili mumpingomo foni idaitana ndiye ndidapita panja kukayankha. Ndili panjapo kulankhula pa fonipo, ndidaona namwaliyu chapakataliko akutonthoza mwana,” akutero Faith.

Maso adali pa namwali, khuku lidali pa foni. Iye samasunthika ndipo pena Brenda akuti amathawitsa diso lake kuti asaphane maso ndi mnyamatayu koma Faith samasunthika.

Izi zidatanthauza kanthu kena mumtima mwa Faith ndipo nkhani yonse idakambidwa patangotha mwezi.

“Titaweruka, ine ndi mchimwene wanga tidaperekeza namwaliyu. Ndinene apa kuti mwana amatonthozayo sadali wake.

“Poyamba Brenda amacheza ndi mbale wanga ndiye pamenepa ndidadziwiratu kuti ndikuyenera kuchita kanthu,” adatero Faith.

Pang’onopang’ono awiriwa adakhazikitsa macheza ndipo Faith sadachedwetse koma kugwetsera mawu oti adzalumikize awiriwa kukhala banja.

“Padatha nthawi kuli zii, za yankho tidakayika koma pa 28 August 2009 ndidangolandira foni kundiuza kuti wagwirizana ndi [mbalume] zomwe ndidamuuza,” adatero Faith wachiwiri kubadwa m’banja la anyamata atatu.

Zonse zatheka pano, awiriwa ndi banja lachitsanzo ndipo atengana kale. n

Related Articles

Back to top button
Translate »