Kudya moyenera n’kofunika

 

Kudya ndi moyo koma woona za kadyedwe koyenera ku Lilongwe University of Agriculutre and Natural Resources (Luanar), Dr Alexander Kalimbira, wati munthu amayenera kudya moyenera kuti akhale ndi umoyo wabwino.

Iye adati kudya moyenera ndi gwero la umoyo wangwiro komanso chitukuko cha dziko.

Kalimbira adati ngati munthu akudya moyenera molingana ndi momwe thupi lake likufunira, amakhala ndi moyo wathanzi ndi wosangalala kotero amagwira ntchito molimbika koma ngati akudya mochepekedwa kapena mopyola muyeso, zotsatira zake ndi matenda osiyanasiyana omwenso akutenga kwambiri miyoyo ya anthu.

Pali magulu 6 a zakudya

“Tikati kudya moyenera sitikutanthauza kuti munthu akuyenera kumadya nsima ndi ndiwo zochuluka ayi koma kudya zakudya zamagulu okwanira pakutha patsiku koma mosadziunjikira. Ngati munthu akudya chakudya chochepa kwambiri komanso chosowekera michere ina, zotsatira zake zimakhala kutupikana, kupinimbira ndi mavuto ena makamaka kwa ana komanso ngati munthu akudya mopyola muyeso, mafuta amachuluka m’thupi ndipo mapeto ake ndi matenda osiyanasiyana monga mtima, kudwala nthenda ya shuga, kuthamanga magazi ndi mavuto ena,” iye adatero.

Iye adati munthu amayenera kumadya chakudya cha magulu onse 6 pamlingo woyenera chifukwa pali zakudya zina michere yake ikachulukitsa m’thupi, imayambitsa mavuto osiyanasiyana. Mwachitsanzo, ngati munthu akuchulutsa kwambiri nsima kapena zakudya zamafuta kwambiri kapenanso za shuga kwambiri, mapeto ake sikelo yake imadzakhala yokwera mopyola muyeso.

“Mmalo modya nsima kapena mpunga wochuluka, anthu ayenera kuonjezera tizakudya ta magulu angapo monga kuika pambali masamba, tinyemba, chipatso ndipo pakutha pa zonsezo, munthu umakhala okhuta koma osatenga michere yochuluka yomwe ikhonza kuunjikana m’thupi n’kuyambitsa mavuto osiyanasiyana,” iye adatero.

Kalimbira adatinso pali tizakudya tina tooneka tapamwamba kwambiri koma tokhala ndi michere yochuluka monga zakumwa zoziziritsa kukhosi zomwe zimakhala ndi shuga wochuluka kotero munthu ukamadya mowirikiza, umakhala pa chiopsezo chonenepa mopyola muyeso komanso zakudya zoterezi, zili patsogolo kwambiri pankhani yoyambitsa matenda a shuga. n

Share This Post