Kulembetsa ndi lero
Kalembera wa Chisankho Chapadera cha pa 17 March chikubwerachi ayamba lero m’madera a aphungu 4 ndi makhansala 9 m’maboma 12 a dziko lino.
Malinga ndi chikalata chomwe bungwe la zisankho latulutsa dzulo, madera onse amene chisankhochi chichitike, kupatula ku Nkhotakota Liwaladzi, kalemberayu aziyamba 8 koloko mmawa mpaka 4 koloko madzulo ndipo adzatha pa 6 February pomwe chisankhocho chidzachitike pa 17 March.

Chikalata chimene wasainira ndi mkulu wa zofalitsa nkhani za MEC a Sangwani Mwafulirwa chati amene adalembetsa pa Chisankho Chachikulu cha pa 16 September safunika kukalembetsanso.
“Pokalembetsa pafunika chitupa cha unzika ngakhale chimene chidatha mphamvu kapena lisiti losonyeza kuti chitupa chidataika,” chatero chikalatacho.
Chisankho Chapaderachi chikuchitika m’madera a aphungu a Nkhotakota Liwaladzi, Dedza Mtakataka, kummwera kwa Blantyre ndi pakati ku Rumphi pomwe makhansala apikisana ku Ighembe ku Karonga, Luwinga ku Mzuzu, Linthembwe ku Dowa, Chilobwe ku Lilongwe ndi ku Msitu ku Mchinji. Makhansala ena apikisana ku Mikongo m’boma la Mangochi, Chanda ndi Chirunga ku Zomba komanso Muonekera ku Thyolo.
Pokonzekera kulembetsa kumeneku, bungwe la zisankho la MEC lidachititsa maphunziro a amene agwire ntchito yolembetsa anthuwa kumadzulo kwa boma la Blantyre. Iwowa adawaphunzitsa kugwiritsa bwino ntchito makina a kalembera wa zisankhowa aja amatchedwa kuti EMD.
Mmodzi mwa makomishonala a MEC a Harry Kanjewe adati kuphunzira kugwiritsa ma EMD n’kofunika chifukwa palibe amene angalembetse osagwiritsa ntchito makinawa.
“Makina amenewa ndi ofunika zedi pa kalembera ameneyu ndipo onse amene azidzagwira ntchitoyi ayenera kudziwa momwe amagwirira ntchito komanso zoyenera kuti munthu alembetse ndiponso azidziwa udindo wawa,” adatero iwo.
A Kanjewe adati akuyembekezera kuti pakhala mavuto, koma akukonzekera kuti mavutowo azithana nawo.
“Tilitu ndi maina okwanira kugwira ntchitoyi dziko lonse ndipo pa malo olembetsera alionse tizikhala ndi makina oposa amodzi kuti ena akasiya kugwira ntchito tizipeza pothawira,” adatero iwo.
Mmodzi mwa amene amaphunzira kugwiritsa ntchito makinawo, Mayi Comfort Sesani adati maphunzirowo adali ofunika chifukwa awathandiza kugwira ntchito ndi anthu a m’madera osiyanasiyana mosavuta.
“M’maderamu tizikakumana ndi anthu a chikhalidwe, chipembedzo komanso kochokera kosiyanasiyana choncho taphunzira kuti tizimvana nawo bwino lomwe powapatsa ulemu ngakhalenso mwa ukadaulo wathu,” adatero iwo.
Ndipo pomwe mtunda wa chisankhochi Wayamba, mabungwe ena ayambapo kale kufika m’midzi kumema anthu kuti akalembetse ndi kukhala ndi Mwayi wovota.
Mwachitsanzo, ku Dedza, mabungwe a Wolrec ndi a Oxfam akulimbikitsa anthu kuti asaphonye Chisankho Chapaderachi.
Iwotu akhala akugwiranso ntchitoyi ku Mtakatakata, Mgawi ndi Nkosini.
Ndipo ku Thyolo, mmodzi mwa makomishonala a MEC a Emmanuel Fabiano adapempha mafumu ndi ena okhudzidwa kuti afalitse uthenga wokhudza chisankhochi.
“Aliyense amene ali ndi zomuyenereza kupikisana nawo pa mpando wa ukhansala ayenera kutero ngakhale sachokera ku deralo koma amene sachokera ku deralo sangakavotereko,” adatero a Fabiano.
Ndipo mmawu awo pokhazikitsa Chisankho Chapaderachi Mayi Annabel Mtalimanja kwa Goliati ku Thyolo komweko adati masiku a kalemberayu ndi 7, kuyambira lero mpaka pa 6 February.
Iwo adati nthawi, sikukhala kusintha dera lovotera.
Ndipo m’mawu awo, DC wa boma la Thyolo a Noel Dakamau adapempha amene akufuna ukhansala m’dera la Thyolo Goliati kuti asamalonjeze zimene si ntchito yawo.
M’dera la Mikongo ku Mangochi, mafumu, mabungwe amene si a boma, atsogoleri a ndale ndi ena onse awapempha kuti azilolerana.
Polankhula ku sukulu ya pulaimale ya Kanjewe adati umodzi ndi wofunika pa chisankhochi.
“Ndife osangalala kuti pa zokambiranazi padali a zipani za Aford, UDF, PP, DPP komanso UTM amene anakwera galimoto imodzi kudzakhazikitsa chisankhochi limodzi,” adatero iwo.
Ndipo a Senior Chief Chowe adati anthu mtima uli dathidathi chifukwa kusowa kwa khansala ku derail kwakhudza kwambiri ntchito za chitukuko ku khonsolo ya bomalo.
“Ndipo monga mfumu, ndipereka mpata kuti opikisana nawo onse akhale ndi Mwayi wochita kampeni kuno,” adatero iwo.
Otolera nkhani: Gomezgani Msiska, Brian Chigumula, Ted Likombola ndi Ayamba Kandodo.



