Nkhani

Kupha nyani sayang’ana nkhope

Listen to this article

Kuyambira pomwe dziko lino lidayamba kukhala ndi ulamuliro wa demokalase (matipate) zinthu pang’onopang’no zidayamba kusokonekera, makamaka pakayendetsedwe ka chuma.

Muulamuliro wa Bakili Muluzi, chuma cha dziko lino chidalowa pansi kotheratu moti njala idalowa; anthu amaswera kumisika ya Admarc koma chimanga kudalibe. Atatenga ulamuliro Bingu wa Mutharika, zaka 5 zoyambirira zinthu zidayamba kusonya ndipo chuma chidayamba kubwerera m’chimake. Koma atasankhidwanso kachiwiri, mtsogoleriyu adatayirira ndipo dziko lidayambanso kulunjika kuphompho. Mmene ankatisiya n’kuti mafuta akusowa m’dziko muno; ndalama zakunja nazo zidasowa; mitengo ya zithu idakwera molapitsa.

Amalawi adaona ngati Chauta wayankha kulira kwawo pamene Mayi Joyce Banda adakhala mtsogoleri wa dziko lino kaamba ka imfa ya Bingu, koma haa! Lero suyu tikumva kuti anthu ogwira ntchito m’boma akungosolola ndalama mmene angafunire, makalaliki akumapezeka ndi mamiliyoni m’nyumba kapena m’galimoto!

M’dziko muno chikuchitika n’chiyani, abale?

Zagwa zatha! Koma Amalawi tikuti tatopa ndi mchitidwe wotibera chifukwa ndalama zikubedwazi zikuchokera kwa anthu osauka amene akukhoma misonkho kuti apeze mankhwala m’zipatala, misewu yabwino ndinso kuti ana awo azipita kusukulu zabwino.

Kwa mtsogoleri wa dziko lino tikuti: chonde nkhani za kuba chuma cha boma zifufuzidwe bwinobwino ndipo lamulo ligwire ntchito ngati mbava zitapezeka. Pajatu amati kupha nyani sayang’ana nkhope!

Related Articles

Back to top button