Nkhani

Mafumu akhumudwa ndi kuvula amayi

Listen to this article

Mafumu komanso anthu m’dziko muno ati ndiokhumudwa ndi zomwe oganiziridwa kuti ndi mavenda m’mizinda wa Lilongwe, Blantyre ndi Mzuzu m’sabatayi povula mbulanda amayi omwe adavala mabuluku kapena siketi zazifupi.

 

Ndemangazi zati apolisi afufuze ndi kugwira omwe adachita chipongwechi.

Malipoti osatsimikizika ochokera ku Mzuzu Lachitatu amati kumenekonso ena adavula amayi ena kumalo okwerera basi ndipo pomwe nthawi imakwana 12 koloko n’kuti apolisi ali balala.

Mafumuwa ati apolisi sakuyenera kunyengerera ndipo yemwe agwidwe akuyenera kukalandira chilango.

T/A Kaomba ya m’boma la Kasungu idati ngati munthu sadavale moyenera ndibwino kuwauza ena amudzudzule, osati kumuvula.

“Zandikwiyitsa. Ngati sadavale bwino akadapeza amayi ena kuti akawadzudzule; uku n’kuchititsa manyazi dziko,” adatero Kaomba.

Senior Chief Tengani ya m’boma la Nsanje yati kuvula amayi silingakhale yankho ngakhale mayiyo atavala molakwika chotani, kotero boma likuyenera kuchitapo kanthu.

“Ife mafumu timalipitsa ovala molakwika. Wina akakuwa mnzake kuti sanavale bwino, mafumu timalipitsa wokuwayo. Otero amalipa nkhuku.

“Koma wina atavula mayi ndiye kuti mlandu uwu sitiweruza; tiuza apolisi kuti akafikitse nkhaniyi kubwalo lamilandu,” adatero Tengani.

Lachitatu mneneri wa boma, Patricia Kaliati adachititsa msonkhano wa atolankhani mumzinda wa Lilongwe momwe adadzudzula mchitidwewu.

Iye adati mayi aliyense yemwe waona zokhomazi awadziwitse.

Related Articles

Back to top button
Translate »