Chichewa

Malingaliro pa malonjezo a Tonse

Listen to this article

Boma lolamula la Tonse Alliance lidalonjeza zambiri panyengo ya kampeni. Padutsa miyezi iwiri tsopano kuchoka pomwe mgwirizanowo udalowa m’boma ndipo manong’onong’o ayamba kale zokhudza malonjezowo. Bungwe la Center for Democracy and Economic Development Initiative (Cdedi) ndi limodzi mwa mabungwe omwe akuwatokosa kuti asaiwale izi. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi mkulu wa bungweli Silvester Namiwa motere:

Tatha miyezi iwiri tsopano mkati mwa ulamuliro wa Tonse Alliance, mukuliona bwanji bomali?

Ayamba bwino koma pali zina zomwe akufunika atakonza msangamsanga chifukwa masiku oyambirira ndiwo amaonetsa kuti paulendowu tiombedwa ndi mphepo yotani. Chachikulu chomwe taonapo nthawi imeneyi ndi uthenga owala ngati maluwa kuchokera kwa mtsogoleri wathu Lazarus Chakwera koma sitidaone ntchito zenizeni tsono polingalira kuti pamathero pa udindo wawo, anthu sadzawayamikira pa uthenga owala ngakhale utachuluka bwanji koma adzaunika kuti miyoyo ya anthu ndi chitukuko cha dziko zasintha motani m’mabanja mwawo n’chifukwa tati mwina tiwatokose kuti asaiwale udindo wawo.

Mukati simudaone ntchito zenizeni kuchoka kwa mtsogoleri mukutanthauzanji?

Namiwa: Amalawi akuyembekezera zambiri

Nthawi ya kampeni ija ankalonjeza zinthu zomwe adzapangire Amalawi akadzapambana. Imene ija idali ngati kontirakiti pakati pa Amalawi ndi Tonse Alliance ndiye Amalawi adapanga mbali yawo povotera Tonse Alliance yomwe ikulamula tsopano. Inoyo ndi nthawi yawo kuti akwaniritse mbali yawo. Amalawitu amasunga zomwe andale amalankhula makamaka pa kampeni ndiye kwinako amangoyang’anira kunjira kuti lonjezo lajuti lija likwaniritsidwa liti kenako akawona kuti kuli ziii, amayamba kutaya chikhulupiliro.

Koma inuyo simukuona kuti masikuwa achepa kwambiri kuti tiyambe kulikumba boma pa malonjezo ake?

Mundimvetsetse pamenepo chifukwa anthu timataya nthawi ndi kuganiza kotero. Sikuti ndikutanthauza kuti kufika lero boma likhale litakwaniritsa malonjezo onse ayi koma kuti pali zina zomwe m’masikuwa zikadakhala zitakwaniritsidwa. Mwachitsanzo, zoti posankha maudindo azidzatengera kuyenerezedwa kwa munthu, mpaka pano sindidaone kasankhidwe kotere kakuchitika ayi. Zoti mkulu wapolisi komanso wa bungwe lothana ndi katangale sizidzakhala mphamvu za pulezidenti kusankha zikadachitika kale m’masikuwa komanso pakali pano amayenera kukhala atayambapo ndondomeko yochepetsera mphamvu za Pulezidenti chifukwa akatenga nthawi, akomedwa ndipo sadzalingalirakonso za lonjezo limenero.

Tatikumbutsani ena mwa malonjezo omwe Amalawi akudikilira?

Malonjezowo alipo ambiri koma mongosefako chabe: Pali lonjezo la feteleza wotsika mtengo wa K5 000 omwe adati aliyense azidzagula mosavuta koma pano akuti angathe kugula ndi anthu 4.5 miliyoni basi. Palinso lonjezo la mswahara wa K15 000 kwa okalamba, ntchito 1 miliyoni kwa achinyamata, kudya katatu patsiku, kukwenza mlingo woyambira kudula msonkho pamalipiro a pamwezi, kutsitsa mtengo wopangira chitupa choyendera kuchoka pa K90 000 kufika pa K14 000, kuchotsa ndalama yolipira ukafuna kukoka madzi kapena magetsi pakhomo komansotu adati pazikhala sabata imodzi yoti munthu aliyense atha kuitanitsa katundu mwaulere kuchoka kunja kwa dziko lino. Mukaona malonjezo awawa ndi wopatsa chikoka kwambiri woti kukhonza kutheka kuti Amalawi adakavota mwaunyinji kuvotera Tonse Alliance kuyembekezera zabwino zoterezi.

Ndikukokereni mmbuyo. Unduna wa za malimidwe udati m’dziko muno muli mabanja 4.5 miliyoni odalira ulimi ndipo akadaulo adati izi zikutanthauza kuti boma likukwaniritsa lonjezo lake?

Ayi! Musasocheletse anthu pamenepo. Tili ndi mavidiyo a nthawi ya kampeni makamaka a wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Saulos Chilima akunena pamsonkhano kuti aliyense azidzagula feteleza wotsika mtengo. Amachita kunyamula thumba la feteleza la makilogalamu 50 kutsimikizira anthu kuti aliyense azidzatha kugula, palibe vidiyo yomwe imanenako za anthu kapena mabanja 4.5 miliyoni ayi. Awowo akadaulo awo muwauze kuti amayenera kubwera ndi maganizo awowo nthawi ya kampeni ija kuti anthu amvetsetse nthawi yomweyo tanthauzo la feteleza kwa aliyense osati kudikira anthu avote kenako n’kumabwera ndi matanthauzo a malonjezo zimenezo n’zosokoneza.

Kaya pangakhale mawu omaliza pamachezawa?

Mawu alipo koma osati okhudza boma kwenikweni ayi koma anthu. Ndikuona kuti tsopano yakwana nthawi yoti mitsutso ikuluikulu ya fedulo ndi yoti aphungu azikambirana m’zilankhulo za kwawo konkuno m’Nyumba ya Malamulo yakwana. Anthu akamasankha aphungu cholinga chawo chimakhala choti azikawayimirira kunyumbayo koma timaona aphungu ambiri akungokhala ngati zikwangwani chitsegulireni mpaka kutseka. Akaoneka kapena kumveka mawu ndiye kuti yafika nthawi yovota pa mutu omwe ukukambidwa. Tili ndi zitsanzo zambiri za aphungu omwe amadziluma kuti atulutse liwu la Chingerezi pakamwa pawo koma amakhala atanyamula nkhawa zambiri za anthu akudera kwawo choncho pamenepa paunikidwe.

Tsekani ndi maganizo anu pa zomwe boma likuyenera kuchita pa malonjezo ndi nkhani mwakamba komalizirako.

Pamene paboma likuyenera kuti liwonetse msanga ndondomeko zomwe lili nazo zokwaniritsira malonjezo ake kuti mwina Amalawi akhazikitse mitima pansi ndi chiyembekezo choti tsiku lililonse zinthu ziyenda. Komanso boma lipereke mpata woti Amalawi ayambirenso kukambirana nkhani iyi ya fedulo ndi yoti aphungu aziloledwa kugwiritsa ntchito zilankhulo zakwathu konkuno ndi kuti pazikhala othandizira kutanthauzira m’nyumbayo kuti aphungu azimasuka.

Related Articles

Back to top button
Translate »