Chichewa

Abwekera tomato wa ufa

Listen to this article

Tomato waufa amasungika kwa zaka ziwiri, mtengo wake ndi golide kale komanso ndiwo zake zimakhala za maonekedwe a pamwamba . Goodfellow Phiri mwini wake wa Environmental Industries amene mwa zina amapanga tomato wa ufa akuti izi ndi zina mwa zinthu zimene zikumuchititsa kuti asabwerere mmbuyo. ESMIE KOMWA adacheza naye motere:

Kodi kuumitsa tomato ndi kumugaya mudayamba liti?

Ntchitoyi ndidaiyamba mu 2012.

Nanga chidakuchititsani kuti muyambe kupanga tomato wotereyu ndi chiyani?

Choyambirira ndimakhala ndi chikhumbokhumbo chopanga chinthu chatsopano choncho nditaona kuti tomato wochuluka m’dziko muno amangoonongeka osakonzedwa choncho kumuumitsa ndi kumugaya kudabwera m’mutu mwanga.

Tomato waufa n’patali

Ndidachita kafukufuku wa mmene ndingachitire izi. Ndidayamba kuyanika tomato ndi kumamugaya ndipo zotsatira zake ndidakhutitsidwa nazo.

Kodi mumagwiritsa ntchito zipangizo zanji?

Basi ndimangoyala pepala panja padzuwa ndi kuduladula tomato ndi kumuyanika. Akauma ndimamugaya n’kumulongeza koma chifukwa choti wina amaonongeka chifukwa cha kusakwanira kwa dzuwa ndimangopanga ochepa chabe.

Ndidachitika mwawi pamene a unduna woona wa za malonda adaonetsa chidwi ndi zimene ndimachita ndi kundithandiza.

Nanga adakuthandizani motani?

Poyamba adatenga tomato wa ufa amene ndimapangayo ndi kukamuyezetsa kubungwe la Malawi Bureau of Standards (MBS) kuti aone michere yake ndi kulipira okha.

Atachoka apo, adandipatsa zipangizo zoumitsira ziwiri zogwiritsa ntchito mphamvu ya dzuwa.

Ndidakaika zipangizozi ku Salima chifukwa kumatentha choncho sizichedwa kukolera dzuwa ndipo masiku atatu okha amakhala wauma.

Kodi tomato amene mumaumitsa panja akusiyana bwanji ndi oumitsa mu zipangizozi?

Kusiyana kwake n’kwakukulu ndithu chifukwa ongoyanika panja amalowa fumbi komanso ntchentche zimaterapo choncho amada pamene wa m’zipangizozi zimene zimaoneka ngati nyumba za pulasitiki amakhala wamaonekedwe a pamwamba ofiira bwino.

Izi zili chomwechi chifukwa amauma m’kanthawi kochepa, salowa fumbi ngakhale ntchentche ndipo saonongeka.

Nanga tomato wa ufayu mumapanga kwa chaka chonse?

Ayi timapanga m’miyezi yotentha kuyambira mu July kulekezera November. Izi zili chomwechi chifukwa m’nyengoyi tomato amachuluka ndipo amakhala wotsika mtengo kwambiri.

M’miyezi inayo timakhala tikugulitsa chifukwa amasowa.

Kodi mumalima nokha kapena mumagula?

Timachita kugula m’misika makamaka ya m’madera mmene mumalimidwa wochuluka ndipo alimi kumeneko akangoona galimoto yathu amathamanga kuti adzagulitse chifukwa timagula wochuluka kwambiri. Upangiri wokwanira kusiyana ndi kuchita patokha.

Anzathu kunjaku zimawayendera chifukwa amabwera pamodzi.

Chomaliza, tiyeni tisamangolimbikira kulima kokha koma tiziganizira zokonza mbewuzi kuti zisamangoonongeka komanso misika ichuluke.

Nanga pa tsiku mumapanga tomato waufa ochuluka bwanji?

Tili ndi kuthekera koumitsa ndi kugaya tomato wokwana makilogalamu 3 000 pa tsiku chifukwa tili ndi zipangizo ziwiri zoumitsira. Ngakhale izi zili chomwechi sitifika pamenepa chifukwa misika yathu idakali yochepa.

Padakalipano tikungopanga wokwana makilogalamu 100 pa tsiku.

Kodi pamenepa mumakhala mwalowetsa tomato wamuwisi wochuluka bwanji?

Timagwiritsa ntchito tomato wokwana makilogalamu 500 chifukwa gawo lalikulu limakhala madzi.

Kodi mumamugula pamtengo wanji?

Nthawi zambiri timamugula pa mtengo wa K150 pa kilogalamu koma imasinthasintha malingana ndi mmene watulukira.

Nanga inu mukamuumitsa ndi kupanga ufa mumagulitsa pa mtengo wanji?

Timamulongeza m’mabotolo a magalamuzi 100 ndi 250. Aang’onowo timawagulitsa pa mtengo wa K1 200 pamene aakuluwo ndi K3 000 botolo lililonse.

Kodi misika mumaipeza bwanji?

Timagulitsa m’sitolo zing’onozing’ono, kwa anthu otidziwa, timatumiza ku Mozambique komanso m’dziko la Germany.

Nanga mungafotokoze mwachidule mmene mumakonzera tomatoyu?

Tikafika naye ku fakitale timasankha okupsa kwambiriyo ndipo wosapsesa timamusunga. Pambuyo pake, timamutsuka ndi madzi a mchere kuti tiphemo tizilombo.

Tikatero timamudula mozungulira ndi kumuyanika pa mathandala amene ali m’nyumba za pulasitiki zija.

Timayenera kumamutembenuza kufikira atauma ndipo akauma timamugaya ndi kumulongeza m’maboto.

Kodi masomphenya anu ndi otani pa bizinesiyi?

Tikufuna titapeza chiphaso kuti tizitha kugulitsa m’sitolo zikuluzikulu ndi kunja, tikhale ndi malo okonzera tomatoyo m’madera onse a m’dziko muno komanso tizilongeza m’milingo yosiyanasiyana kuti tizitha kufikira anthu onse.

Nanga anthu amene akufuna kuyamba bizinesiyi mungawalangize motani?

Kuyamba chinthu kuti chifikepo munthu amakhala walimbana nacho makamaka yokonza zinthu za mtunduwu. Ndikupempha anzanga amene ali ndi khumbo loteleri kuti tibwere pamodzi ndi kumachitira limodzi ndipo tikatero ntchitoyi ipita patsogolo, misika yochuluka ipezeka, tikhala ndi zipangizo.

Related Articles

Back to top button