Amanga opezeka ndi mankhwala popanda chilolezo
Apolisi ku Mponela m’boma la Dowa amanga abambo atatu omwe adapezeka ndi mankhwala osiyanasiyana omwe amagulitsa mgolosale yawo.
Mneneri wa polisi ya Mponela a Macpatson Msadala atsimikiza zakumangidwa kwa abambo atatuwo ndipo ati akawonekera kukhothi posachedwa.

Izi zachitika patangopita miyezi yochepa mtsogoleri wadziko lino a Peter Muthalika atalamula kuti anthu makamaka ogwira ntchito zachipatala asamachite bizinesi yachipatala kapena yogulitsa mankhwala.
A Mutharika adanena izi mchitidwe woba mankhwala utakula m’zipatala zaboma koma ogwira ntchito zachipatala sadagwirizane n’chiletsocho.
A Msadala ati abambo atatuwo ndi a Frank Phillip a zaka 27, a Holyce Mayembe azaka19 ndi a Happy Mayembe azaka 18 onse ochokera mmudzi mwa Kawere kwa Senior Chief Mponela.
“Mlandu wawo ndiwogulitsa mankhwala popanda layiasensi zomwe malamulo salola. Matekitivi apolisi adakatsimikiza atapanga chipikisheni,” adatero a Msadala.
Iwo ati ena mwamankhwalawo ndi mapilitsi 4 000 a ibuprofen, ka capsules 3000 a Amoxicillin, 3 000 a indocmethacin, 3000 a metronidazole, 4000 a phenobarbital, 2 000 a magnesium, 1 000 a paracetamol, 1 000 a aspirin, 1 000 a metrodozole, 2 000 a sulfamethoxazole, 1 000 a cotrim.
Ena ndi mapilitsi 1 000 a chlorpheniramine, 1 000 a prednisolone, 2882 a altbendozole, 2 040 a LA, ma capsules 4 700 a amoxicillin, 1 792 a rifampicin, 1 400 a phonoxymethyl omwe adalibe makalata ake.
Kadaulo pazaumoyo a George Jobe ati mpofunika kuti boma liyambe kuchitapo kanthu mmalo momangolankhula chifukwa ambiri mwamankhwalawo amatuluka mzipatala zaboma.
“Kulankhula kokha sikungaphule kanthu, mankhwala akubedwa pafupifupi m’boma lililonse. Kumafunika kuti zomwe adalankhula a Muthalika ziyambe kugwira ntchito,” adatero a Jobe.
Mtsogoleri wotsutsa boma mNyumba ya Malamulo a Simplex Chithyola Banda adauza mbali yaboma kuti ikonze vuto lakusowa kwamankhwala mzipatala.



