Nkhani

Mapemphero a mvula aliko lero

Listen to this article

Pamene ng’amba yadzetsa chikaiko choti Amalawi akhoza kukolola zochepa chaka chino, mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika lero akhala nawo pa mapemphero a mvula amene achitike mumzinda wa Lilongwe.

Malinga ndi mlangizi wa Mutharika pa za chipembedzo Timothy Khoviwa, mapempherowo akhalanso othokoza Mulungu pa zochitika za chaka chatha.

Mutharika led Malawians in prayer
Mutharika led Malawians in prayer

Mapempherowo akachitikira ku Bingu International Conference Centre (BICC) pansi pa mfundo yaikulu yakuti ‘Kudzipereka kwa Mulungu posinkhasinkha mtendere ndi chitukuko cha dziko’.

“Tikakhalanso tikupempha Mulungu kuti atipatse zokolola zokwanira mu 2016. Kuli atsogoleri a mipingo yosiyanasiyana. Iyinso ndi nthawi yakuti a zipembedzo zosiyanasiyana akhalire pamodzi,” adatero Khoviwa.

Mapempherowa akudza pomwe nthambi yoona za nyengo idati kudula kwa mvula kwa sabata ziwiri kwadzetsa chikaiko pakati pa alimi ndi Amalawi ena onse.

Mneneri wa nthambiyo Ellina Kululanga adati kudulaku kwadza chifukwa cha nyengo ya El Nino imene ikuchititsa kuti madera a m’chigawo cha kumwera mugwe ng’amba pomwe kumpoto ndi pakati chiyembekezo chilipo kuti mvulayi igwa bwino.

Malinga ndi kafukufuku wa nyuzipepala ya The Nation, madera ambiri mvula siyikugwa bwino zimene zingachititse kuti zokolola zichepe. Izi zikudza pomwe m’chaka cha 2015 zokolola zidatsika ndi makilogalamu 30 pa makilogalamu 100 alionse chifukwa cha vuto la madzi osefukira amene adakokolola mbewu zambiri.

Related Articles

Back to top button