Nkhani

Mavenda akwiya ndi kukwera kwa lenti

Listen to this article
Ena mwa mavenda wotemetsa nkhwangwa pamwalawo
Ena mwa mavenda wotemetsa nkhwangwa pamwalawo

Malonda adayima kwa maola angapo mumsika waukulu wa Zomba pamene mavenda mumsikawu adatseka zipata kuti akuluakulu a khonsolo ya mzindawu asalowe kukadulitsa ziphaso.

Chimene chidatsitsa dzaye ndi chikalata chimene khonsolo ya mzindawu yatulutsa chonena kuti yakweza mitengo yolipirira lenti munyumba zimene mavendawa amachitira malonda asadakambirane kaye ndi akuluakulu oyang’anira mavendawa.

Chikalata chimene mkulu wa mzindawu Ali Phiri adasayinira pa 23 June 2014 chidafotokoza kuti kuyambira pa 1 July 2014, mitengo yatsopano ili motere: amalonda ogulitsa zitsulo (hardware) lenti yawo yakwera kuchoka pa K5 200 kufika pa K7 800; kwa anthu a magolosale yachoka pa K5 400 kufika K8 100; kwa a malo odyera yachoka pa K7 200 kufika K10 800; kwa ometa komanso omanga tsitsi mitengo yachoka pa K3 600 mpaka K6 000 ndipo kwa ogulitsa nyama mitengo yachoka pa K3 000 mpaka K4 500.

Pachifukwachi, pa 18 July 2014, mavendawa adalembera khonsoloyi kuti mitengoyi yakwera kwambiri ndipo adapempha kuti awatsitsire. Mwachisoni, pa 26 July 2014, mavendawa adatutumuka atalandira kalata kuchoka kukhonsoloko kuti khonsoloyi siliyokonzeka kutsitsa mitengoyo ndi kutsindika kuti mavevenda amene akuona kuti sakwanitsa kulipira mitengo yatsopanoyi atuluke mumsikamo kuti khonsoloyo ilowetsemo anthu ena amene azikwanitsa kulipira.

“Ndikudabwa kuti akhonsolowa angotiuza kuti mitengo ya lenti yakwera koma sadatifotokozere eni akefe. Kodi zinthu zimakhala chocho?” adafunsa Ayatu Chidothe, wapampando wa mavenda mumsikawu.

Chidothe adati ndi wachisoni kwambiri ndi mmene akuluakulu a mzindawu akugwirira ntchito zawo ndi mavendawa masiku ano chifukwa akutaya pangano limene adagwirizana lakuti azipangira zinthu limodzi pakusintha kwina kulikonse mumsikawo.

Mkuluyu adaulua kuti pamene msikawu udapsa ndi moto zaka zingapo zapitazo khonsolo ya Zombayi idakana kuwapatsa chipukuta misozi ponena kuti ilibe ndalama. Pa chifukwa ichi, mavendawa anamemana ndi kupita kukakumana ndi mtsogoleri wakale wa dziko panthawiyo malembu Bingu wa Mutharika amene adawauza kuti iye sakwanitsa kuwapatsa ndalama koma kuwamangira msika watsopano.

Mavendawo atemetsa nkhwangwa pamwala kuti satuluka mumsikawo kufikira pamene khonsoloyo idzamve madandaulo awo ndi kutsitsa mitengoyo.

Kuonjezera apa, mavendawa anena kutinso khonsoloyi iwafotokozere bwino mmene ndalama zimene zimatoleredwa mumsikawu zimagwirira ntchito chifukwa ngakhale khonsoloyo ikukweza mitengo chotero uve mumsikamo ndi wandiwe yani chifukwa zinyalala ndi zithaphwi ndi zochuluka popeza pamatenga nthawi yaitali kwambiri kuti khonsoloyi izakonze msikawu.

Related Articles

Back to top button
Translate »