Nkhani

Mayi athokoza ataomboledwa

Listen to this article

Maness Thom wa Zaka 65 wathokoza bungwe losakhulupirira kuti kunjaku kuli Mulungu komanso mphamvu za mizimu ina la Association of Secular Humanism (ASH) pomuimirira mpaka kupulumuka pankhani yomwe amamuganizira kuti ndi mfiti.

 

Poyankhula ndi Msangulutso Lachitatu lapitali, Thom adati samakhulupirira kuti angadzakhalenso paufulu poganizira mmene anthu ndi abale ake adamuperekera m’manja mwa apolisi ku Kawale mumzinda wa Lilongwe komwe amachokera.

Iye adagwidwa m’chaka cha 2011 ndipo khoti lidamupeza wosalakwa mu 2012 ASH itamumenyera nkhondo kubwalolo ndipo adati tsopano akukhala popanda vuto ndi abale akewo.

“Adandigwira kunyumba kwanga mmawa uku akunditonza kuti ndine mfiti ndipo kuti ndidapha munthu m’matsenga, komanso ndimaphunzitsa ana ufiti. Ndidalephera kudziteteza chifukwa ena adali atayamba kundikankha ndi kundimenya uku akundikokera kupolisi,” adatero mayiyo.

Adaonjeza kuti atafika kupolisiko adamutsekera ndi kumutsegulira mlandu wochita za ufiti ndipo adagona komweko. Iye adati chikaiko chake chidakula chifukwa nthawi ya kukhoti itafika, samadziwa chomwe akadayankha chipanda mkulu wa ASH George Thindwa kubwera poyera kuti amupezera omuimirira.

Thom adati Moses Kwayimba, yemwe adakaperekera umboni mukhothi woti iye ndi mfiti, ndi mbale wake koma sagwirizana kuyambira kale ndipo wakhala akumulengera milandu yosiyanasiyana koma imasowa umboni.

Thindwa wati bungwe lake silifuna kuti anthu azizunzika powaganizira kuti ndi mfiti. Iye adati bungwelo latulutsa anthu oposa 80 omwe adali mundende Za m’dziko muno komanso lamangitsapo anthu ena omwe adazunzako anthu oganiziridwa kuti ndi afiti.

Thom akuti akukhala mwamtendere ndipo anthu onse ku Kawale komwe amakhala kuphatikizapo akumpingo kwawo adamulandira.

Related Articles

Back to top button