Nkhani

Mfumu yadzikhweza ndi za fetereza wa AIP

Listen to this article

Amfumu a Chidzalo a zaka 71 omwe dzina lawo ndi a Moffat Lamulani Mlenga a m’boma la Dowa adzikhweza pothawa ngongole ya zipangizo zotsika mtengo zaulimi (AIP) yomwe anthu amawavutitsa nayo.

Mneneri wapolisi ya Dowa a Alice Sitima wati pali chikhulupiriro choti amfumuwo adalandira ndalama kwa anthu osiyanasiyana powalonjeza kuti adzawapatsa chiphaso chawo AIP ikayamba.

A Sitima akuti nthawi itakwana, a Mlenga adapereka chiphaso chawo kwa munthu mmodzi ndipo adatenganso cha akazi awo mowazembera n’kupatsa munthu wina ndipo akhala akuvutitsidwa ndi anthu ena otsalawo.

Koma iwo akuti mfumuyo siyidasiye kalata yopereka zifukwa zodziphera.

“Zikuoneka kuti adalandira ndalama kwa anthu osiyanasiyana koma adangothandizako awiri okha ndiye enawo amamuvuta poti msika wa AIP uli mkati panopa ndiye adangoganiza zodzipha,” adatero a Sitima.

Iwo adati pa 1 December 2023, banja la a Mlenga lidapita kumunda pomwe iwo amagwira ntchito zina pakhomo koma pobwerera kumundako, banjalo lidapeza a Mlenga atadzimangirira ku denga.

Mng’ono wa amfumuwo a Patrick Chidzalo a zaka 44 ndiwo adathamanga kukadziwitsa apolisi ndipo adatengera amfumuwo kuchipatala cha Dowa komwe adatsimikiza kuti amwalira kaamba kobanika.

Aka si koyamba kuti mafumu agwe m’chipwirikiti pa nkhani za makuponi. Mu January, mfumu ina idamangidwa itapusitsa anthu ake 10 potenga zitupa zawo n’kukagula fetereza mwachinyengo m’boma la Nkhata Bay. Ndipo ku Machinga wina adapezeka ndi zitupa 268 pomwe ku Karonga, mwezi omwewo mkulu wina adamangidwa atapezeka ndi zitupa 22 koma anali asanakagule fetereza.

Izi zikutsatira kumangidwa kwa ogulitsa zipangizo za AIP atatu ndi mlonda mmodzi pa msika wa Smallholder Farmers Fertiliser Revolving Fund of Malawi ku Nkhotakota.

Lipoti likuti nthambi yolimbana ndi katangale ya Anti-Corruption Bureau (ACB) lidalandira lipoti pa 16 November 2023 kuti akuluakuluwo amakakamiza anthu ogula zipangizozo kupeleka ndalama zapadera.

Kalata yochokera ku ACB yosainidwa ndi mneneri wa nthambiyo a Egrita Ndala ikuti kafukufuku atachitika, padapezeka umboni wokwanira kuti katangaleyo amachitikadi pamsikawo.

“Potsatira kafukufuku wathu, pa 4 December 2023, ACB idamanga a Gift Mkanda ogulitsa zipangizo, a Maria Chilinda ogulitsa zipangizo, a Lovemore Kandu ogulitsa zipangizo ndi a Wilson Masanjala mlonda,” udatero kalatayo.

Pamsonkhano wa atolankhani wokonzekera kutsegulira AIP, nduna ya za malimidwe a Sam Kawale adalonjeza kuti m’pulogalamu ya 2023/24, boma silinyengerera aliyense ogwidwa ndi katangale m’pulogalamuyo.

Iwo ankayankha funso loti pulogalamu ya chaka chatha siyidayende bwino mwa zina kaamba ka katangale pomwe ogulitsa amakakamiza alimi kuti azipereka K5 000 yapamwamba kuti apeze mpata wogula.

Chaka chino, alimi 1.5 miliyoni ndiwo akuyembekezeka kupindula m’pulogalamu ya AIP kuchoka pa alimi 2.5 miliyoni chaka chatha ndipo a Kawale adalengeza posachedwapa kuti alimi omwe agula kale sadafike theka la alimi omwe ali pamndandanda wopindula.

Related Articles

Back to top button
Translate »