Miyezi 30 kwa ogona ndi ng’ombe
Bwalo la Chitipa Senior Resident Magistrate, Lolemba pa 14 July 2025, lidagamula bambo wina wa zaka 24 a James Mtambo, kuti akakhale ku ndende kwa miyezi 30, atapezeka wolakwa pa mlandu wogona ndi ng’ombe.
Bwalo la Chitipa Senior Resident Magistrate, Lolemba pa 14 July 2025, lidagamula bambo wina wa zaka 24 a James Mtambo, kuti akakhale ku ndende kwa miyezi 30, atapezeka wolakwa pa mlandu wogona ndi ng’ombe.

Izi zidachitika mu mwezi wa March chaka chino pamene bamboyo adali ku nyumba kwake m’bomalo.
Wachiwiri kwa m’neneri wa polisi ya Chitipa, a Sergeant Mathews Mfune, adati mlanduwo udamvedwa kudzera kwa woimira boma pa milandu, Mayi Dorah Mhango, yemwe adauza bwalolo kuti patsikulo, a Mtambo adapezereredwa ndi anthu a m’mudzimo akugonana ndi ng’ombe yomwe adaimangirira ku mtengo.
Iwo adauzanso khotilo kuti panthawiyo n’kuti mwini wake wa ng’ombeyo atadziwitsa kale anthu okhala m’mudzimo za kusowa kwa ng’ombe yake.
Tsono atayambapo kafukufuku wake m’mudzimo, iwo adamupeza bamboyo akuphwetsera mkhuto wake pa chiwetocho. Bamboyo adayesera kuthawa pa malopo koma pamapeto pake, adagwidwa ndi anthuwo omwe adapita naye ku polisi ya Chitipa.
Poonekera ku bwalo la milandu, iwo adaukana mlandu wogona ndi ng’ombe zomwe zidachititsa kuti a kumbali ya boma abweretse mboni zinai kuti apereke umboni wawo ndipo pamapeto, adamupeza wolakwa.
A Mhango, adapempha khotilo kuti lisamvere chisoni bamboyo chifukwa mlanduwo unali waukulu. Koma bambo Mtambo anayesetsa kulilira bwalolo kuti limpatse chigamulo chofewa popeza anati anali akudwala.
Ngakhale ananena izi, khotilo silinamve dandaulolo chifukwa bamboyo analephera kutulutsa umboni wochokera ku chipatala wosonyeza za nthenda yomwe ankadwala.
Popereka chigamulo, woweruza mlanduwo, a Ephraim Chikwakwa, adamugamula miyezi 30, yoti akakhale ku ndende ndi cholinga chopereka phunziro kwa ena omwenso anali ndi maganizo oipawo.
A James Mtambo amachokera m’mudzi mwa Yesaya m’dera la T/A Mwaulambia m’bomalo.



