National News

‘Mnzanga ndiye adandipezera’

Nthawi zina ndi bwino kumakhala ndi anzako omwe angakuthandizire kuti upeze zinthu zabwino m’moyo wako. Izi ndi zomwe zidamuchitikira Emmanuel Tembo yemwe adapeza njole yake Mary Thomas m’njirayi.

Emmanuel anati atamaliza maphunziro ake a sekondale mu 2019 adaganiza zochita maphunziro a shipping and logistics ku Soche Technical College mu mzinda wa Blantyre.

Iye anati panthawiyi adali ndi chibwenzi chomwe samadziwa kuti chidalinso ndi chibwenzi chokhazikika ndiye adatsetsa chibwenzicho mu November 2019.

“Nditafika ku nyumba mu December, mnzanga wina Maxwell Rogers anandiuza kuti kwa Ndenguma kuli mkazi, tidapitako kukamuona komatu padali vuto limodzi makolo a mkaziyo samamulola kuti azituluka ku mpanda kwawo. Limodzi ndi Maxwell tidatumanso mnzathu wina Yosefe yemwe amakhala moyandikana naye kuti ndikumanaye ndipo adamuuza kuti ngati ndikufunadi ndipite kwawoko pa 12 January 2020,” adatero iye.

Ndipo atapita adagwetsa Chichewa koma zidatenga miyezi itatu kuti amuvomere. Atamuitanitsa kuti akaonekere kwa makolo ake adamulandira bwino ndi kumuuza kuti akabwere ndi abale ake kudzamangitsa banja.

Iye anati ngakhale adachita kumufunira ndi mnzake komatu mwa Mary adapezamo mkazi wa khalidwe labwino, wofatsa komanso msangalatsi wa moyo wake popeza nthawi zina amatha kukhala ku Tete kapena ku Beira m’dziko la Mozambique kwa chaka kukasaka ndalama koma sakhala ndi nkhawa.

Mary adati poyamba amakaikira kuti mwina Emmanuel angofuna kumuvula koma ataona kuti akumukakamira adaona kuti amuvomere kukhala mwamuna wake.

Iye anati: “Pofuna kuona kuti analidi ndi cholinga cha banja ndidamuyendetsa kwa miyezi itatu n’kumulola. Atafika kwathu, ndidadabwa kuti makolo anga omwe saonetsa mano wamba kwa anthu adamusekerera ndi kumulandira. Atapita adandiuza kuti uyu ndiye mwamuna wondiyenera.”

Iye adati amaona Emmanuel ngati mphatso yomwe Mulungu wakumwamba adamupatsa chifukwa ndi iyeyu tsiku limakhala labwino kwambiri. “Akakhala kutali ndisaname mtima umawawa. Ndimamulola kupita ku Mozambique chifukwa choti timafuna tizikhala ndi moyo wabwino n’chifukwa chake ndakwanitsa kuongolera kumanga nyumba ziwiri,” adatero iye.

Awiriwa adamangitsa chinkhoswe pa 15 January 2022 ndipo ali ndi mwana wa mwamuna wa zaka 4, Dumisani.

Tembo ali ndi zaka 33 ndipo amachokera kwa Fulukiya pomwe Mary Thomas wa zaka 26 amachokera kwa Ndenguma, onse kwa T/A Malemia m’boma la Nsanje.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button