Mpofunika kuthana Ndi nyongolotsi
Kale alimi a m’gulu la ulimi wa ng’ombe la Chilangoma kwa T/A Kuntaja m’boma la Blantyre samapindula ndi ulimiwu kaamba ka tizilombo monga nyongolotsi ngakhalenso nkhupakupa makamaka nyengo ya mvula ikafika.
Malingana ndi wapampando wa gululo a Harry Zimpita, tizilomboti timapha kwambiri tiana komanso ng’ombe zambiri zazikulu zimaoneka zoonda ndi zonyentchera.
Tsopano ndi nkhambakamwa chifukwa mothandizidwa ndi alangizi alimiwa adapanga gulu limene padakalipano lili ndi alimi a ng’ombe za nyama oposa 90 ndi cholinga choti azithana ndi tizilomboti komanso matenda pamodzi.
“Patokha zimativuta chifukwa mankhwala ndi okwera mtengo koma alangizi athu atatitsegula m’maso ndi kumasonkherana ndalama zogulira ngati gulu kuti tizitha kutsatira ndondomeko yonse ulimiwu udaphweka chifukwa zidayamba kuoneka za thanzi ndipo kufa kwa ana kunachepa,” adafotokoza motero.
Kupatula kumwetsa mankhwala opha nyongolotsi, mlangizi wa m’deralo a Emmanuel Chikaonda adati adadzusanso dipi thanki imene inkangokhala osagwira ntchito kuti azithana ndi nkhupakupa zimene zimasautsanso kwambiri ng’ombe makamaka m’dzinja.
Malingana ndi mkulu wa zaulimi wa ziweto m’boma la Kasungu a Jacob Mwasinga, nyongolotsi ndi nkhupakupa zimaswana kwambiri mu nyengo ya mvula kaamba ka kuchuluka kwa chinyontho.
Chifukwa cha ichi, iwo adati alimi amayenera kupereka mankhwala opha nyongolotsizi ku ziweto zawo kumayambiriro kwa nyengo ya mvula ndi kumapeto kwa nyengoyi.
“Kumwetsa koyambiriraku kumathandiza kuti ziweto zipite m’nyengo ya mvula zilibe nyongolotsi pamene kumwetsa kachiwiri kumathandiza kuti tichotse nyongolotsi zonse zimene ziweto zatenga m’nyengo ya mvula.
“Izi sizikutipatsa malire opereka mankhwalawa ku ziweto chifukwa tikuyenera kudzipasanso nthawi ina iliyonse ngati zagwidwa ndi tizilomboti,” iwo adatero.
A Mwasinga adati zizindikiro zoonetsa kuti ziweto zagwidwa ndi tizilomboti ndi monga kutsegula m’mimba,kuimika ubweya, kuonda, kutupa kwa kunsi kwa khosi ndipo nthawi zina kutsokomola.
Iwo adafotokoza kuti alimi sakuyenera kulekelera chifukwa nyongolosi zimayamwa magazi komanso zimalimbirana chakudya ndi ziweto choncho mmalo moti chakudya chigwirentchito m’thupi la chiweto chimathera mu tizilomboti.
Kuonjezera apo, iye adati nyongolosizi zikachuluka zimatha kutseka matumbo ndipo mapeto ake chiweto chimafa.
“Nyongolotsi zina monga za nkhumba zimayenda m’thupi mwa munthu amene wadya nyama yosapsa ya chiwetochi mpakakukafika ku ubongo. Mapeto ake munthu amatha kupenga misala,”iye adatero.
Mkulu wa nthambi ya za maphunziro a zaulimi ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resiurces (Luanar) Jonathan Tanganyika adaonjeza kuti ng’ombe ndi mbuzi nazo kwambiri nyengo ya mvula ikafika zimagwidwa ndi nyongolosi za m’chiwindi.
Iye adafotokoza kuti kawirikawiri izi zimachitika ziwetozi zikamadya m’malo monga m’madambo.
“Malo abwino ambiri odyetsera ziweto m’nyengoyi amakhala alimidwa choncho zimakadya kudambo kumene kumapezeka kwambiri nkhono zimene zimanyamula nyongolotsizi.
“Ziweto zikamadya udzu m’madambowa zimadyera limodzi nkhono choncho nyongolotsi zimalowa m’chiwindi mwa ziweto,” adafotokoza motero.
Malingana ndi mkuluyu, alimi akhoza kugwiritsa ntchito piperazine kumwetsa ziweto monga nkhumba ndi nkhuku pofuna kupha nyongolotsizi pamene Ranox amagwiritsidwa ntchito kumwetsa ng’ombe ndi mbuzi.
Werengani patsamba la chitatu kuti mudziwe zambiri za dip.