Friday, August 19, 2022
  • About Us
  • ImagiNATION
  • Rate Card
  • Contact Us
The Nation Online
Advertisement
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
No Result
View All Result
Home Chichewa

Muva: Kutsitsimutsa anthu mukuimba

by Dailes Banda
30/08/2015
in Chichewa
2 min read
0
Share on FacebookShare on TwitterShare on WhatsAppShare on LinkedinLinkedinShare via Email

Lero Lamulungu akuyembekezeka kukakhazikitsa chimbale chake cha Messiah 1 ku Mzuzu pa Boma Park. Kumeneko kukakhala oimba osiyanasiyana odziwika m’Malawi muno. DAILES BANDA adacheza ndi Donnex Muva kuti amudziwitsitse mkuluyu, yemwe akuti cholinga chake n’kutsitsimutsa anthu kudzera mu nyimbo. Adacheza naye motere:

Akhazikitsa chimbale chake lero: Muva
Akhazikitsa chimbale chake lero: Muva

Tikudziweni achimwene.

Ndine Donnex Muva ndipo ndimachokera m’mudzi mwa Kajani kwa Inkosi Kampingo Sibande m’boma la Mzimba. Ndili ndi zaka 32 zakubadwa, ndili pabanja ndipo ndili ndi ana atatu.

 

Mbiri ya maphunziro anu njotani?

Ndayenda sukulu zambiri kaamba ka bambo anga omwe ndi abusa, koma mayeso anga a Sitandade 8 ndidalembera ku Chihami m’boma la Nkhata Bay ndipo sekondale ndidaphunzira ku Chintheche m’boma lomwelo.

Nditamaliza sekondale ndidachita mwayi woyamba ntchito ku Chipiku koma pakadalipano ndikugwira ntchito kubungwe la Solar Aid Malawi.

 

Mudayamba bwanji kuimba?

Kuimba ndidayamba ndili wachichepere kwambiri, makamaka kaamba ka ubusa wa bambo anga. Panthawiyo ndinkaimba mukwaya ya kumpingo kwathu. Kuimba kwenikweni ndidayamba m’chaka cha 2009 pomwe ndidatulutsa chimbale choti Nthawi ya Manna Inatha.

Chaka chino ndikuyembekezeka kukakhazikitsa chimbale changa cha Messiah 1 ku Mzuzu ku Boma park pa 30 August. Kumeneko kukhalanso oimba osiyanasiyana odziwika m’Malawi muno.

 

Zomwe mwakwaniritsa pamoyo wanu ndi ziti?

Chachikulu chomwe ndakwaniritsa ndi kubweretsa anthu kwa Mulungu kudzera mu nyimbo komanso kukhala ndi zimbale ziwiri si chinthu chapafupi chifukwa kupanga chimbale pamalowa ndalama zambiri.

 

Pali zopinga zotani zomwe mwakumanapo nazo?

Zopinga ndiye zilipo, choyamba ndi mchitidwe woba nyimbo moti ndikunena pano anthu ayamba kale ‘kubena’ nyimbo zanga. Mchitidwewu umabwezeretsa kwambiri mmbuyo anthu oimbafe. Chachiwiri ndi kusowa kwa chithandizo popanga chimbale. Monga ndanena kale, ndalama zimalowa zambiri pantchito yapanga chimbale, zomwe oimba ambiri sitingakwanitse patokha ndipo timafuna chithandizo kuchokera kwa makampani akuluakulu monga zimakhalira kumaiko ena.

 

Oimba anzanu muwauza zotani?

Pakhale chikondi pakati pathu osati kuponderezana. Ndi mtima wofuna kukhala pamwamba nthawi zonse womwe ukuononga oimba ambiri m’dziko muno.

 

Nanga omwe akuyamba kumene?

Kuimba ndi mphatso ndipo si aliyense amatha. Anthu ambiri osatha kuimba akuonongetsa maimbidwe m’dziko muno; ena ndi aja amangotenga nyimbo zoti adaimba kale anthu ena n’kumangozisintha. Ili si luso koma kuba.n

Previous Post

Abusa ku HIH ndi zina

Next Post

A day at a circumcision site

Related Posts

Patrick sakubwerera mmbuyo pa chikopa
Nkhani

Patrick Mwaungulu ndi katakwe pokankha chikopa

July 24, 2022
Chilima: Change the mindset toward development
Nkhani

A Chilima abwera poyera

July 1, 2022
Nkhani

Achilima awachepetsera mphamvu zaulamuliro

June 24, 2022
Next Post

A day at a circumcision site

Opinions and Columns

My Turn

Diagnostic tech cost on patients

August 19, 2022
Business Unpacked

Why public debt should worry every patriotic Malawian

August 18, 2022
Rise and Shine

How to triumph in interviews

August 18, 2022
My Turn

Making briquettes at Malasha

August 15, 2022

Malawi-Music.com Top10

Trending Stories

  • Court snubs tenants on govt houses

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • ‘Blantyre derby could have fetched more’

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Why graft cases stall

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • World Bank protests K14bn ICT contract

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Govt appoints university working committee

    0 shares
    Share 0 Tweet 0

  • Values
  • Our Philosophy
  • Editorial policy
  • Advertising Policy
  • Code of Conduct
  • Plagiarism disclaimer
  • Disclaimer
  • Privacy Policy
  • Terms of use

© 2022 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation

© 2020 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

This website uses cookies. By continuing to use this website you are giving consent to cookies being used. Visit our Privacy and Cookie Policy.