Nandolo mpatali

 

Ubwino wa nandolo si uli pa kupeza ndalama zochuluka kokha komanso zina zambiri, watero mkulu woona za mbewu za m’gulu la mtundu wa nyemba ku Bvumbwe Research Station, Richard Andasiki.

Andasiki adati pambali poti mbewuyi ndi imodzi mwa mbewu zimene alimi angaphe nazo makwacha ochuluka, ilinso ndi chakudya chabwino chomanga thupi, imabwezeretsa chonde m’nthaka, siyivuta kulima, ndi yosavuta kusunga ngakhalenso kusamalira pamene ili mmunda. Iye adatinso mitengo ya nandolo ndi nkhuni zabwino.

“Nandolo amabwezeretsa chonde m’nthaka munjira ziwiri. Poyamba masamba ake akayoyokera m’munda, amaola mosavuta ndipo amakhala manyowa amphamvu. Kachiwiri, mizu ya nandolo imakhala ndi tizinthu tooneka ngati totupa tomwe timakhala ndi tizilombo  tobwezeretsa michere yotchedwa nitrogen m’Chingerezi yomwe ndi yofunika kwambiri ku mbewu,” iye adatero.

Nandolo ali ndi phindu lochuluka

Andasiki adafotokoza kuti chifukwa cha kubwezeretsa chonde m’nthakaku, mbewu zina monga chimanga zimapindula.

Iye adati nandolo salira zipangizo zochuluka monga feteleza komanso safuna chisamaliro chochuluka n’chifukwa chake amachita bwino ngakhale abzalidwe pamodzi ndi chimanga kotero safunanso chisamaliro chapadera chifukwa pamene mlimi akusamalira chimanga chake, amakhala akusamaliranso mbewuyi koma ngati wabzalidwa payekha, chachikulu ndi kupalira basi.

Isaac Mpunga, mmodzi mwa alimi a nandolo a m’boma la Nsanje adati mbewuyi ndi yomwe yachita bwino kwambiri kudera kwawoko ngakhale mvula inadukiza.

“Nandolo amafuna  mvula  nthawi yochepa n’chifukwa chake amatha kukula komanso kubereka mvula italeka kotero ndi mbewu yothandiza,” iye adatero.

Ngakhale izi zili chomwechi, alimi a nandolo chaka chino adandaula kuti mbewuyi yayamba ndi mtengo otsika kwambiri kusiyana ndi chaka chatha.

Jonath Goliath, mmodzi mwa alimi omwe amalima mbewuyi mochuluka ngati bizinesi yake, wa m’boma la  Neno wati izi ndizokhumudwitsa kwambiri chifukwa mtengowu sukupereka chiyembekezo chilichonse.

“Padakalipano, nandolo ali pa K100 pa kilogalamu chonsecho chaka chatha adayamba pamtengo wa K500 pa kilogalamu ndipo adachita kutsika n’kufika pa K250 pa kilogalamu. Zikudabwitsa kuti akachoka pamenepa afika pati,” adatero iye.

Goliath adadabwa kuti ngakhale boma lidaika mtengo wotsikitsitsa wa nandolo kukhala K320 pakilogalamu, ogula akugula pa K100. “Mitengo yopendereza alimife ogulawa akuitenga kuti?” adadabwa iye.

Mlimiyo adati zaka za mmbuyomu, mbewu ya nandolo ndi yomwe idali ndi phindu  koma panopa siikulongosoka zomwe zikusowetsa alimi pothawira.

Arthur Ngwende, woona za malonda kukampani ya Farmers Organisation Limited (FOL) imalimbikitsa alimi kugwiritsa ntchito mbewu zamakono komanso mankhwala othandiza kuti nandolo akule bwino ndiponso imatha kudziwa za momwe misika ya mbewuyi ikuyendera, wati alimi akhonza kudikirira kaye kufikira nandolo wawo atauma bwinobwino.

“Nandolo wangokololedwa kumene kotero amakhala wolemera kwambiri chifukwa amakhala akadali ndi madzi choncho zikhonza kutheka kuti ogulawa akuchitira dala kumagula pamtengo woterewu n’chifukwa chake alimi sakuyenera kuthamangira,” iye adatero.

Ngwende adatinso dziko la India, limene limagula mbewuyi kwambiri m’dziko lino, layamba kulima lokha, choncho silikugulanso nandolo wochuluka ngati kale.

Andasiki adavomereza kuti alimi akuyeneradi kusunga kaye mbewuyi kuti ayambe aona momwe mitengo ikhalire miyezi ikubwerayi.

Iye adati kuti asungike bwino komanso kwa nthawi yaitali, choyambirira amuumitse kufikira chinyontho chisapyole ndi 12 peresenti ndipo akatero amuthire mankhwala chifukwa kupanda kutero amafumbwa.

“Mankhwala ake ndi ofanana ndi omwe timathira kuchimanga ndipo mlimi akathira mankhwalawa, amayenera kuika m’matumba abwino. Akatero, asunge pamalo pabwino posafika chinyontho komanso asanayambe kusanja matumba, pansi ayalepo zinthu monga matabwa kuti matumbawo asagunde pansi,” iye adatero. n

 

Share This Post