‘Nandolo wa makono ndiye yankho’

 

Ngakhale mitengo ya nandolo siyinali bwino kwenikweni chaka chatha, Jonath Goliath wa m’boma la Neno akuti adachita mphumi popeza adagulitsa pa mtengo wabwino ndipo izi zidamupatsa mphamvu kulima wochuluka kusiyana ndi zaka zonse kuti aphenso makwacha koma mphuno salota, akuti sakudziwa ngati lotoli likwaniritsidwe chaka chino. ESMIE KOMWA adacheza naye motere:

Kodi chaka chatha ulimi wa nandolo udayenda bwanji? Alimi ambiri adaliratu…

Kunena zoona, zidandiyenderadi chifukwa ndinagulitsa pa mtengo wa K600 pa Kilogalamu pomwe nthawi imeneyo anthu ambiri amagulitsa pa mtengo wa K250 pa kilogalamu ndipo ndidapeza ndalama zochuluka ndithu n’chifukwa chake  ndidapanga chisankho cholima nandolo wochuluka koma momwe zilili panopa, ndayamba kukhumudwa.

Goliati: Sindinakolole nandolo kuti aume bwino

Chidachitika n’chiyani kuti mugulitse motero pomwe ena amagulitsa motsika?

Ndidachita mwayi kugulitsa ku bungwe la Shire River Basin Management komwe panopa ndizokaikitsa ngati atigulenso potengera kuti panopa nandolo wayamba ndikutsika mtengo kwambiri.

Simunapange nawo mgwirizano kuti chaka chino akuguleninso?

Dongosolo lidali lotero koma mkatikati mwa mgwirizano wathuwu, kwapezeka kuti zinthu zayamba kusokonekera, zikuoneka ngati apeza alimi ena omwe awagule chaka chino kotero ndidangozisiya mkumayembekezera kuti mwina chaka chino mitengo ikhala yabwino koma panopa ndi momwe mavenda ayamba kugulira, sindikuona tsogolo. Izi zikutibwezera mmbuyo ife alimi chifukwa tidakakhala kuti timagulitsa mwabwino m’zaka zonse, bwenzi miyoyo yathu ikutukuka.

Ndi zinthu zanji zomwe mungaloze kuti mudapeza kuchokera ku ulimiwu?

Ndalama yomwe ndakhala ndikupeza kuchokera ku ulimiwu yatukula pakhomo panga ndithu chifukwa ndidamanga nyumba, ndidagula njinga yamoto, ndidapeza ziweto monga mbuzi ndi nkhuku moti chaka chino ndi momwe ndalimira ndimayembekezera zinthu zopotsera pamenepa ndithu. Kuonjezera apa, ndalama yotsalayo ndidagwiritsa ntchito kulimitsa m’munda komanso kugula mbewu yamakono yotchedwa Mwayiwathu Alimi ndi mankhwala othandizira kuti achite bwino otchedwa Nyonga Pack.

Nandolo amafunanso mankhwala?

Inde ndipo ndi yemwe amachita bwino kwambiri kusiyana ndi kungolima mwachisawawa moti inenso zaka za mmbuyozi ndimangolimapo koma ndazindikira chaka chathachi kutabwera a kampani ya Farmers Organisation Limited(FOL)kudzatiphunzitsa. Ndidagula mbewuyi ndi mankhwalawa  ndipo wachita bwino kwambiri kusiyana ndi zaka zonse.

Tafotokozani ubwino wobzala mbewu ya makonoyi komanso kugwiritsa ntchito mankhwalawa paulimiwu.

Ubwino ndiye ndi wosayamba ndipo ndawuona chifukwa maberekedwe ake ndi osiyana kwambiri ndi njira zachikale. Kuonjezera apa, nandolo wake amakhala wosiririka m’maonekedwe. Chaka chatha, nandolo adaonongeka ndi mbozi komanso maluwa amangoyoyoka zomwe zidapangitsa kuti asabereke kwambiri koma chaka chino zimenezi sizinachitike ndipo ndakhulupirira kwambiri kuti mankhwalawa ndiwothandiza chifukwa malo omwe sindinathire, sanachite bwino ngati momwe wachitira winayu. Padakalipano, sindinayambe kukolola ndikudikira amalizike kuuma koma ndili ndi chiyembekezo kuti ndikolola wochululuka kwambiri.

Kodi kulima nandolo mwa bizinesi mudayamba liti?

Kulima kwenikweni ngati buzinesi ndidayamba mu 2012 pomwe ndidayamba kudziyimira pandekha.

Chinakukopani kwambiri mu ulimiwu n’chiyani?

Kwambiri ndimafuna mbewu yomwe ikhonza kumandibweretsera ndalama zochulukirapo ndipo nditaganiza bwino ndidaona kuti nandolo ndikhonza kupindula naye.

Kusonyeza kuti zaka za mmbuyozo mitengo yake inali yabwino kwambiri?

Tikhonza kutero kusiyana ndi momwe zilili panopa.

Nanga m’zaka zonsezi, ndi mavuto anji omwe mwakhala mukukumana nawo mu ulimiwu?

Mavuto omwe ndimakumana nawo ndi monga timbozi ndimanenato komanso kuyoyoka kwa maluwa zomwe zimandipangitsa kuti ndisamakolole mokwanira koma panopa momwe ndazindikira za kugwiritsa ntchito mankhwalawa komanso mbewu ya makono, ndi  mbiri yakale. Dandaulo ndi ndalama yogulira makamaka mitengo ikakhala yotsika motere chifukwa sitipeza phindu loti tikhonza kukagulira nyengo ikubwerayi.

Mawu anu owonjezera ndi otani?

Ndikufunitsitsa titathandizidwa kuti tipeze misika yabwino chifukwa zikumatiwawa kuti alimi tikutaya thukuta komanso ndalama zathu pachabe koma popanda phindu zomwe zikutipangitsa kuti tizikhala anthu olimbikira koma osatukuka momwe zimayenera kukhalira. n

Share This Post