Ndidakamira kufunda nawo ambulera’

 Padali pa 5 February 2014, kunja kuli mvula yamphamvu ya mabingu pomwe Devlin Nazombe kapena kuti ‘Mmisiri Wopanda Zida’ yemwe amagwira ntchito ngati muulutsi kunyumba youlutsa mawu ya Angaliba komanso amaongolera zochitika monga zikwati ndi zina adakumana ndi mkazi wake Gloria Muhiwa.

Ndipo Nazombe yemwe tsiku lina adaona koyamba Gloria atafunda ambulera kuphelera mvulayo.

Devlin ndi Gloria pa tsiku la ukwati wawo

Apatu Nazombe sakadachitira mwina koma kumuimitsa namwaliyo n’kumupempha kuti afunde nawo.

“Ndidamuimitsa kuti ndifunde nawo chifukwa ndidali ndikunyowa kwabasi. Nditamuimitsa adanyogodola koma sindidaimve, ndidakakamira kufikira pomwe adandiloleza kufunda nawo,” adalongosola Nazombe.

Komatu Nazombe sadapitire kufunda nawo ambulera kokha chifukwa adayamba kumupempha Gloria nambala yake ya lamya.

“Gloria adakanitsitsa kuti sangandipatse nambalayo. Koma ndidamukakamiza kuti chabwino angotenga nambala yanga ndipo adailemba m’manja kuti akakafika kwawo akaisunge,” Nazombe adatero.

Iye adawonjezera kuti atafika posiyana adamuchondelera namwaliyo kuti ayankhulane naye madzulo atsikulo chifukwa adali ndi chikaiko chachikulu.

Koma Nazombe adati padadutsa sabata ziwiri asadamuyankhule ndipo adaiwalanso zoti adapereka nambala.

“Tsiku lina ndidaona uthenga woti ndiimbire munthu lamya ndipo nditamufunsa kuti ndi ndani adati Gloria, ndidabalalika kwambiri mpaka kufunsa kuti wakuti? Ndiye adandilongosolera kuti ndidamupatsa nambala yanga. Koma nditakumbukira, tidayamba kucheza,” iye adatero.

Patadutsa kanthawi awiriwo akucheza, Nazombe adamufunsira mkaziyo yemwe akuti adavuta kwambiri kuti amulole, komabe pamapeto pa zonse adavomera ndithu.

“Kuchokera nthawi imeneyo takhala tikukumana ndi zokhoma zochuluka monga chibwenzi kutha n’kudzayambiranso; anzake amamuuza kuti sindingamukwatire chifukwa ndine wotchuka ndipo anthu otchuka sakhala ndi mkazi mmodzi koma chosangalatsa n’choti Gloria samazitengera zonsezo,” Nazombe adalongosola.

Koma awiriwo omwe amanga ukwati wawo pa August 31 pa mpingo wa South Lunzu CCAP ndipo madyelero adali ku Grace Garden ku Machinjiri, mumzinda wa Blantyre akulangiza anthu onse omwe ali m’chikondi kuti asamamvere zokamba za anthu komanso chikondi chao chizikhala chotsogoza Mulungu kut mzonse azikula.

Iwo adati akakumana ndi vuto lililonse amakhala pansi ndikukambilana modekha kuti wolakwa avomereze ndikupepesa ndipo zikatha amagwada pansi ndikumupempha Mulungu kuti awayanjanitse.

Awiriwa amakhala ku Machinjiri mumzinda wa Blantyre ndipo Gloria amagwira ntchito ku sitolo za PEP komanso ali ndi salon komwe amamanga anthu tsitsi.

Nazombe amachokera m’mudzi mwa Kandota, T/A Phambala, m’boma la Ntcheu pomwe mkazi wake ndi wa m’mudzi mwa Njoloma, T/A Chikumbu, m’boma la Mulanje

Share This Post