Anatchereza

 Kodi nditani?

Gogo Natchereza

Ndine mtsikana wa zaka 25 ndipo ndakhala pa chibwenzi ndi mnyamata wina kwa zaka zinayi.

Mnyamatayu ali ndi nyumba yake ndipo akugwira ntchito yabwino pa kampani ina yopanga mafuta wophikira mu mzinda wa Lilongwe.

Tidagwirizana kuti tidzakwatirana, koma mnzanga ndikamufunsa za banja amangozengereza.

Kumuuza kuti apite kwathu akaonekere amangoti ndidzapitabe mpaka zaka n’kumatha.

Gogo, kodi pamenepa nditani popeza mnyamatayu ndimamukonda ndi mtima wanga wonse?

JPJ

Lilongwe

JPJ

Nkhaniyi siyachilendo. Atsikana ambiri amadandaula kuti anyamata adawauza kuti adzawakwatira, koma akuchulutsa njomba.

Mnyamata wofuna banja sasowa. Sazengereza mwayi wokaonekera kwa makolo a mtsikana ukapezeka.

Anyamata ambiri safuna banja. Amangofuna kugona ndi atsikana moti chakumtima kwawo chikapwa amawasiya n’kupeza ena kumene kuli kulakwa.

Muunikeni bwino bwenzi lanu kuopa kudzanong’oneza bondo mtsogolo. Paja amati mtsinje wa tinkanena udakathera m’siizi.

Gogo Natchereza

Makolo ake akukana

Ndine mtsikana wa zaka 23 ndipo ndili ndi mwana mmodzi.

Mnyamata wina adandiuza kuti akundifuna chibwenzi ndi cholinga choti adzandikwatire mtsogolo ndipo ndidalola.

Koma makolo ndi abale ake amamukaniza kuti asakwatiwe ndi mtsikana wa mwana moti panopa zochita za bwenzi langa sindikuziona bwino.

Ndikamuimbira foni nthawi zina sayankha. Ndikamutumizira uthenga pa WhatsApp umaonetsa kuti waona, koma

 sayankha.

Gogo, mutu wanga wazungulira nditani?

APA

APA

Usadandaule, ungozivomereza. Makolo ena amaletsa ana awo kukwatiwa ndi atsikana oti adaberekapo kumene kuli kulakwa.

Anthu awiri akakondana zenizeni saona zoti wina ali ndi mwana kapena ayi.

Apa zikuonetsa kuti mnyamatayo wamvera zonena za makolo ake. Choncho kutha kukhala kovuta kuti chibwenzi chanu chipitirire.

Limba mtima, mudzapeza mnyamata wokukondani posatengere kuti mudaberekapo.

Usada nkhawa. Chachikulu ndi kudekha. Sunga khosi mkanda woyera udzavale.

Natchereza

Share This Post