‘Ndimakasiya ndalama ku banki’

Abdul-Majid Ntenge amagwira ntchito ku Emmanuel International, koma kwambiri amadziwika ngati mtolankhani.

Mu 2017 adanyamuka ulendo kukasiya ndalama ku Ned Bank m’boma la Mangochi. Ali komweko adaona mtsikana wogwira ntchito m’bankimo. Wosalala, timano take ta mpata, wa msangala komanso wochezeka, uyo adali Ruckaya Dickson Jasiya.

Abdul-Majid ndi bwenzi lake Ruckaya

Akadatani Abdul? Iye adapanga ulendo wina kuti acheze ndi namwaliyo koma mbalume zonse zidaomba khoma. “Adandikana,” adatero. “Ndidayendera kangapo komabe adakanitsitsa.”

Mbuto ya kalulu idakula ndi tadzaonani, kusatopa kwa Abdul kudapangitsa kuti Ruckaya afike pomuzolowera ndipo adamulola kumapeto kwa chaka chathachi.

“Pali zambiri zomwe ndinganene pa Abdul koma chimodzi chomwe ndidziwa mkuti adalola momwe ndilili. Amaganiza za ine asadapange chilichonse. Sindikufuna ndisiyanitse Chikondi chake ndi cha ena koma mwamuna uyu amandikonda,” adatero Ruckaya.

Naye Abdul adati namwaliyo ndi wowopa Mulungu, wokonda kupemphera, wofatsa, wakhalidwe labwino komanso ndi wachikondi.

“Komanso ali ndi mfundo zomwe amatsatira pamoyo wake zomwe ine ndimazikonda kwambiri,” adatero.

Ukwati wa awiriwa uchitika pa 4 May chaka chino ndipo ukachitikira pa Mkambiri Lodge m’boma la Mangochi.

Abdul ndi wa m’mudzi mwa Ntagaluka, mfumu yayikulu Chowe m’boma la Mangochi pomwe Ruckaya kwawo ndi kwa Katuli, mfumu yaikulu Katuli m’boma lomwelo. n

Share This Post