Chichewa

‘Ndinkapita ku ntchito’

John Paul Kayuni ndi mtolankhani panyumba youlutsa mawu ya Zodiak mumzinda wa Lilongwe.

Udali m’mawa wa pa April 12, m’chaka cha 2018 pomwe ankathamangira kuntchito, nthawi imeneyo n’kuti akukhala kwa Biwi kudera lotchedwa Gonjetso pomwe adakumana ndi Phalles Stambuli. Pakadalipano Stambuli amagwira ntchito ku wailesi ya CAN.

“Ndimathamangira ndithu chifukwa ndidali nditachedwa, kenako ndidaona mtsikana akubwera kumbuyo kwanga, nayenso adali pa changu ndithu.  China chake chidandiuza kuti ndichepetse liwiro kuti ndimudikire. Aka kadali koyamba kukumana,” adalongosola Kayuni.

Awiriwo adayendera limodzi kuchokera pamenepo kukafika pa malo okwerera basi amene amangotchedwa kuti pa Share World pakati pa Kawale ndi Mchesi pomwe adakwera limodzi minibasi.

Kayuni ndi Phaless adamangitsa ukwati mwezi watha

Pomwe Kayuni adali akuthamangira  ku ntchito, naye Stambuli ankathamangira kokachita mayeso a ntchito omwe ankachitikira kusukulu ya sekondale ya Bwaila.

“Tidasiyana pa Cashbuild pomwe ine ndidatsikira, ndipo ndidamufunsa kuti andipatse nambala yake ya foni kuti tizilumikizana chifukwa tidacheza bwino kwambiri tsiku limenelo. Kuchokera apo Phalles adakhala mnzanga,” adatero Kayuni.

Ndipo naye Stambuli adati adamukonda Kayuni kuchokera pa tsikuli.

“Ndidagwa naye m’chikondi nditangomuona, ndisadadziwe za dzina ndi mbiri yake,” adatero Stambuli.

Pa nthawiyi n’kuti Kayuni ali wosweka mtima chifukwa padali patangopita miyezi yochepa ubwenzi womwe adali nawo ndi mtsikana wina utangotha, ndipo adalibe maganizo okhalanso pa ubwenzi wina.

“Nditha kunena kuti ndidali wosweka mtima. Ndidapitirizabe Kucheza ndi Phalles, ndipo nthawi yonseyi sadandiuze kuti nayenso ndi mtolankhani, moti ndikamacheza naye ndinkakonda kumufotokozera za zomwe zachitika,” adatero Kayuni.

Popeza onse adali mbeta, pang’onopang’ono Kayuni adayamba kugwa m’chikondi.

“Kukongola kuli apo, ndidagwa m’chikondi ndi Phalles kaamba ka mtima wake wabwino komanso wodekha. Koma ndidali ndi mantha kuti ndimuuze. Ndidali ndi mantha kuti ndikamuuza mwina sagwirizana nazo ndipo kuti chinzake chomwe chidalipo chisokonekera,” adalongosola Kayuni.

Koma tsiku lina, Kayuni adalimba mtima ndipo adamuuza; koma Stambuli sadamulole tsiku lomwelo.

Komabe masiku atadutsa, Stambuli adamulola ndipo ubwenzi wawo udayamba.

Nawo akapasule adayamba kulowererapo.

“Posakhalitsa padayamba kutuluka nkhani, mtsikana wina, adamulembera Phalles uthenga wa pafoni womuuza kuti kunyumba kwanga kumabwera mtsikana kudzagona usiku ndipo kuti asamale chifukwa ndine wokonda akazi,” adatero Kayuni.

Awiriwo akhala pa ubwenzi kwa zaka ziwiri ndipo adakwatirana pa 1 August 2020. Ukwati wawo adadalitsira pa mpingo wa Mtima Woyera Parish mzinda wa Lilongwe.

Ukwatiwu unkayenera kukhalapo pa 1 May chaka chino koma udalephereka chifukwa kwa mliri wa Covid-19.

Pomwe Stambuli amachokera ku Chiwamba, kwa mfumu Chimutu, m’boma la Lilongwe, Kayuni amachokera m’mudzi mwa Namuyemba, Mfumu Mwabulambia, m’boma la Chitipa.

Pakadalipano awiriwo akukhalira ku Area 25, mumzinda wa Lilongwe.

Awiriwo akulangiza omwe ali pa chibwenzi kuti asamagwedezeke ndi zomwe anthu akunena.

“Chofunika kwambiri ndi kudziwana awirinu. Mamveramvera amapasula. Ngakhale padali mavuto awa tinakhalabe limodzi kwa zaka zoposa ziwiri,” iwo adatero.

Related Articles

Back to top button