Nkhani

Njovu ipha mlenje

Listen to this article

Tsoka sasimba. Akanadziwa mlenje sakadapita kunkhalango ya Liwonde kukasaka nyama mozemba masiku apitawo.

Patrick Maya, wa zaka 52, ndipo amachokera m’mudzi mwa Chipala, Senior Chief Kawinga m’boma la Machinga, koma adasamukira m’mudzi mwa Wadi, Senior Chief Liwonde komwe amakhala ndi banja lake adafa njovu itamuponda.elephants

Malinga ndi mchimwene wa Maya, Maxwell Makina, iye adali ndi chizolowezi chosaka nyama mozemba pogwiritsanso ntchito agalu ake  m’nkhalango  ya Liwonde.

Makina adati pa tsiku la tsokali, Maya adalowa mkhalangoyi komwe sadabwererenso.

Iye adati ngakhale nkhani ya kusowa kwake idawapeza abalewa m’mudzi mwa Chipala  laMulungu lapitali, akukhulupilira kuti mlenjeyu adaphedwa pa Khirisimisi.

“Thupi lake lidapezeka Lamulungu pa 27 December, litaonongeka kale moti tidangosunga patchire pomwepo,” Makina adatero.

Wachiwiri kwa mneneri wapolisi kuchigawo cha ku m’mawa Otilia Kumanga watsimikiza za imfayi.

Related Articles

Back to top button