Nkhani

‘Osakondera odya nawo K6.2 biliyoni’

Listen to this article

Bota layamba kuwira mumphika wa K6.2 biliyoni yothandiza polimbana ndi matenda a Covid 19 yomwe ikumveka kuti idatafunidwa ndipo akuluakulu a m’makhonsolo adaimitsidwa ntchito kuti afufuzidwe.

Koma mabungwe oima pa okha ati kuimitsidwa kwa akuluakulu a m’makhonsolowo sikukununkha kanthu chifukwa nduna zina za boma nazo zikuyenera kuimikidwa ntchito.

Wapampando wa gulu la mabungwe omwe si aboma la National Advocacy Platform (NAP) Benedicto Kondowe komanso woyendetsa ntchito za bungwe loona za ufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) Luke Tembo adanena izi m’misonkhano iwiri yosiyana.

Kondowe adati n’zachisoni kuti boma likufuna kumata phula anthu m’maso kuti likupangapo kanthu poimitsa akuluakuluwo pomwe anthu enieni ofunika kufufuzidwa akadali m’mipando.

“Mwachitsanzo, Dr [Charles] Phuka adachotsedwa pampando wawo kukomiti yoona za Covid pomwe mdindo mnzawo Khumbize Kandodo Chiponda yemwenso ndi nduna ya zaumoyo akadali pomwepo.

“Ndimayesa kuti kulephera kwa komiti ndi kulephera kwa awiri onsewo? Kupatula apo, tikumva za a Kondwani Nankhunwa okha za maalawansi nanga mamembala ena omwe ambiri ndi nduna zikuti bwanji? Apapa pakubisidwa chilungamo,” adatero Kondowe.

Pomwe Tembo wati chomwe Amalawi akufuna ndi lipoti lonse la momwe K6.2 biliyoni ya Covid 19 idayendera apo ayi kukhala zionetsero za mnanu m’dziko muno.

Iye watinso HRDC ikufuna Nankhumwa abweze K3.6 miliyoni yomwe adavomera kuti adatenga kumphika wa Covid 19 ngati maalawansi ndipo kenako atule pansi udindo wake otsogolera mbali yotsutsa boma.

“Sitikusekerera munthu ayi chifukwa ndalama zomwe zaonongekazo zidali zopulumutsira anthu odwala koma taona momwe anthu apululukira pakatipa pomwe ena amadya ndalama,” adatero Tembo.

Iye adati ndi K3.6 miliyoni boma likadatha kugula masilinda a mpweya wa Oxygen 36 kapena ma flowmeters 16 zomwe n’zofunika kwambiri pothandiza anthu omwe akubanika ndi Covid 19.

Lamulungu lapitali, mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera adati pakuchitika kalondolondo wa K6.2 biliyoni ndipo atha mwezi umodzi koma wachenjeza kuti aliyense amene adzakodwe mukangaude wosolola kuthumbali adzamangidwa.

“Kalondolondoyo akuunika lipoti la komiti ya Covid 19 ndipo gawo lachiwiri lidzakhala kulondoloza momwe Kwacha iliyonse idagwirira ntchito. Pamapeto pa kalondolondo ameneyu, aliyense yemwe adzapezeke ndi banga adzamva kuwawa,” adatero Chakwera.

Kupatula akuluakulu a m’makhonsolo, boma lidaimitsanso akuluakulu ena a nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi komwenso kukuoneka kuti ndalama zankhaninkhani zidazembetsedwa.

Pachifukwachi, Tembo wati HRDC imenya nkhondo yoti nthambiyo ifufuzidwe momwe ndalama za ngozi zogwa mwadzidzidzi zammbuyomo zimayendera osati kuthera pa K6.2 biliyoni ya Covid 19 basi.

Related Articles

Back to top button