Nkhani

Teketeke popereka zikalata

Listen to this article

Mzinda wa Blantyre mudali teketeke m’sabatayi pomwe bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidalandira zikalata za omwe akufuna kudzaimira nawo pachisankho cha pa 2 July.

Ngakhale anthu amene adaloledwa m’chipinda choperekera zikalatazo ku Sunbird Mount Soche adatsata ndondomeko zopewera matenda a Covid-19, chipwilikiti chidali panja pomwe anthu samakhala motalikana.

Chakwera adzaima limodzi ndi Chilima

Mwa anthu 9 omwe amayenera kupereka zikalata zawo, atatu okha ndiwo adavomerezedwa kutero.

Lazarus Chakwera motsatana ndi Saulos Chilima adzaimira mgwirizano wa Tonse Alliance momwe muli zipani 9. Peter Kuwani adzaimira Mbakuwaku Movement for Development motsatana ndi Archibald Kalowong’oma pomwe Peter Mutharika motsatana ndi Atupele Muluzi adzaimira mgwirizano wa zipani zaDPP ndi UDF.

Smart Swira, Phunziro Mvula, Chikomeni Chirwa, Shaibu Mustafa, Khwechani Nkhoma ndi Levelend Kaliya adakanika kukhala nawo pamndandandawo kaamba ka zolinga zina, monga kulephera kukwanitsa zofunika.

Mutharika ndi Muluzi atapereka zikalata zawookhawo

Atamaliza kupereka zikalata zake, Chakwera adati nthawi yosintha zinthu tsopano yakwana ndipo adadzudzula kwambiri MEC posayendetsa bwino chisankho cha pa 21 May chaka chatha, chimene bwalo lamilandu lidagamula pa 3 February chaka chino kuti n’chosavomerezeka.

Kuwani, yemwe adasonyeza mkwiyo chifukwa chisankho cha 2019 sichidabale zipatso, adayamikira womutsatirayo posafooka.

Ndipo m’mawu ake, Mutharikaadati ngakhale akudziwa kuti adapambana chisankhocho, ali ndi chikhulupiriro chonse kuti iye apambana pachisankho chikudzachi chifukwa  akuimalimodzi ndi Muluzi yemwe akudziwa bwino za chitukuko.

Polankhula ndi opereka zikalatazo payekhapayekha, wapampando wa MEC Jane Ansah adati pochita kampeni, atsogoleriwo ayenera kubwera ndi njira zatsopano zochitira kampeni. Malinga ndi matenda a Covid-19, boma lidati anthu asakhale oposa 100 malo amodzi, zimene zingakhudze kampeni yomwe idayamba pa 2 May.

Padakalipano, akadaulo a za ndale ena aikapo mlomo pa momwe chisankhochi chikuyendera.

Ndipo kadaulo wina, Humphreys Mvula adachenjeza kuti ngakhale mwayi wa misonkhano uli wovuta malingana ndi nkhani ya Covid-19, zipanizi zisabwekere pa momwe zidachitira pa chisankho cha 2019 koma kuti apeze njira zodzigulitsira kwa anthu.

“Taona mtima wodzichepetsa kwambiri mwa atsogoleri a ndale chifukwa zomwe anthu ambiri amakayika kuti zingatheke, zatheka ndiye kwatsala n’kuchilimika kukopa anthu kuti zidzayende bwino pachisankho,” adatero Mvula.

Oyendetsa ntchitoza mgwirizano wa mabungwe okhudzana ndi zisankho wa Malawi Electoral Support Network (Mesn) Andrew Kachasu adati zateremu zakhala bwino chifukwa zasonyeza kuti zokonzekera chisankho zikuyenda koma iye adati zipani zipewe mtopola.

“Zikamatere ndiye kuti zikuyenda bwino tsono chomwe ndingapemphe n’choti popanga kampeni, zipani ziyike mtima pogulitsa mfundo zawo osati kunena za ena kapena kulankhula monyodola ena ayi,” adatero Kachasu.

Kadaulo pa za malamulo Nandini Patel adatanthauzira mgwirizano ngati ubale omwe zipani ziwiri kapena koposa apo zimapanga n’cholinga choonjezera mwayi wawo wopeza mavoti ochuluka pachisankho.

Pachisankho chomwe bwalo lidatembenuza, chipani cha Mutharika yemwe adaimira DPP adapeza mavoti 1 940 709 kuimilira anthu 38 pa 100 aliwonse; Chakwera wa MCP adapeza 1 781 740 kuimilira anthu 35 pa 100 aliwonse; Chilima wa UTM Party adapeza mavoti 1 107 369 kuimira anthu 20 pa 100; pomwe Muluzi wa UDFadapeza 235, 164 kuyimira anthu 4 pa 100.—Otolera: STEVEN PEMBAMOYO ndi WISDOM CHIROMBO

idaphwanya malamulo a dziko pakayendetsedwe ka chisankhocho.

Iwo anati malamulo a dziko lino samapereka mphamvu kwa aliyense kufuta zotsatira za chisankho. Zidaoneka kuti zotsatira za chisankho zina zidafutidwa ndi utotowa Tippex komanso zikalata za zotsatira zina zidali zochita kukopera zomwe zidali kuphwanya ufulu wa anthu.—Otolera nkhani: STEVE PEMBAMOYO ndi WISDOM CHIROMBO

Related Articles

Back to top button
Translate »