Chichewa

Tetezani ana ku BP

Chimodzimodzi akulu, ana nawo amakhala pachiopsezo cha matenda othamanga magazi choncho makolo akuyenera kuwateteza, watero mkulu wa pa chipatala cha Moyowathanzi m’boma la Lilongwe Henry Ndhlovu akuti.

Iye adafotokoza kuti ana omwe amakhala pa chiopsezo chodzadwala matendawa mtsogolo ndi oyambira zaka zitatu kulekezera 6 kapena 8.

“Kawirikawiri ana oterewa amakhala omwe adabadwa masiku asadakwane komanso  ndi sikero yotsika. Matenda a imphyo ndi a mu mtima amakolezeranso vutoli ku ana,” iye adatero.

Masewero olimbitsa thupi ndi ofunika kwa ana

Kwa ana omwe abadwa opanda mavutowa, Ndhlovu adati zinthu monga kunenepa kwambiri, kudya zakudya za mafuta, mchere ndi shuga wambiri kumaika ana pachiopsezo chodzadwala matendawa mtsogolo.

Mkuluyu adaonjeza kuti kusachita masewero olimbitsa thupi ndi gwero lina la matenda othamanga magazi ku ana.

“Ana omwe adabadwa ndi mavuto ena mu impso kapena mtima, masiku awo asadakwane kapena ndi sikero yochepa, ziwalo zawo sidzigwira ntchito moyenera.

“Zotsatira zake, magazi sayenda bwino monga momwe amayenera kuchitira,” iye adatero.

Mkuluyu adafotokoza kuti makolo akuyenera kutenga gawo lalikulu mwachitsanzo kupewa zinthu zomwe zikhoza kuchititsa kuti mwana abadwe ndi mavutowa.

Kuonjezera apo, iye adati makolo apewe kuwapatsa ana chakudya chokhala ndi shuga, mchere ndi mafuta ochuluka.

“Aziwalimbikitsa ana awo kuchita masewero olimbitsa thupi komanso azikawayezetsa matendawa,” adakwangula motero.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button