Samalani ndi chitopa

Kuchokera ku phindu la ulimi wothirira, Catherine Bamusi wa m’boma la Blantyre adaganiza zogulako nkhuku zachikuda kuti zizimupatsa manyowa, ndiwo ngakhalenso ndalama akazingwa.

Iye adayamba ndi nkhuku 6 chaka chathachi ndipo pamene amalowa m’chaka chino zidali zitachulukana kufika 50.

“Ndili mkati modyerera, nkhuku zanga zidagwidwa ndi chitopa ndipo padakalipano ndilibe ndi imodzi yomwe chifukwa zonse zidafa,” adandaula motero Bamusi.

Pezani phindu lochuluka ku nkhuku zachikuda pozipatsa katemera

Marcus Twayah wa m’boma la Mulanje akuti chitopa chimamusautsa chaka chilichonse koma khama pa ulimiwu ndi lomwe limamuchititsa kuti zikafa, agule nkhuku zina ndi kuyambiranso kuweta.

“Padakakhala kuti palibe chitopa, bwenzi ndikutakata kwambiri chifukwa ulimiwu ndi waphindu.

“Ndimakwanitsa kuyambiranso chifukwa siulira zambiri ngati momwe umakhalira ulimi wa nkhuku za mazira ndi zanyama,” adabwekera motero mlimiyu.

Malingana ndi mphunzitsi wa zaulimi wa ziweto ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) Jonathan Tanganyika, matenda a chitopa ndi oopsa kwambiri.

Iye adati awa ndi matenda omwe amapha nkhuku zambiri zachikuda m’dziko muno.

“Matenda ena akagwira nkhuku amapha koma sangafanane ndi momwe chitopa chomwe ena amachitchula kuti  chideru chimasakazira.

“Matendawa amagwira nkhuku panthawi ndi kupha zambiri ndipo pamadutsa miyezi ingapo asadabwerenso,” iye adafotokoza motero.

Malingana ndi mphunzitsiyo, matendawa amayamba ndi mavayilasi choncho chifukwa choti tizilombo tamtunduwu timavuta kupha, palibe mankhwala omwe amachiza chitopa chikagwa m’khola.

Iye adachenjeza alimi kuti asamanamizidwe kuti pali mankhwala a chitopa kapena zitsamba zochiza matendawa.

“Alimi ayenera kuteteza nkhuku zawo ku matendawa pozipatsa katemera wa matendawa monga I-2 yemwe akupezeka m’sitolo za vetenale za m’dziko muno.

“Katemerayu ndi wotsika mtengo ndipo alimi akuyenera kumapatsira nkhuku zawo m’miyezi inayi iliyonse kuti zizitetezeka,” adatero Tanganyika.

Mphunzisiyu adati m’botolo la katemerayu mumakhala madontho 200 omwe mlimi amayenera kupatsira ku nkhuku 200.

Iye adati mlimi amayenera kudonthetsera m’diso limodzi la nkhuku iliyonse.

Kadaulo wa ulimi wa ziweto m’boma la Blantyre Edwin Nyondo adati katemera wina wotetezera ku chitopa ndi lasota.

“Alimi amayenera kumwetsa nkhuku katemerayu miyezi itatu iliyonse komanso anapiye asanakwane sabata ziwiri,” adafotokoza motero.

Tanganyika adati katemera ndi njira yokhayo yotetezera nkhuku zachikuda ku matendawa m’dziko muno chifukwa n’zosatheka kuziweta m’njira yoti zisamasakanikirane ndi nkhuku zina ngati momwe amachitira m’maiko ena.

Mphunzisiyu adati izi zili chomwechi chifukwa nkhuku zachikuda m’dziko muno zimayendayenda kusakasaka zakudya.

Kuonjezera apo, iye adati nyengo ino ndiyamaukwati komanso zinamwali choncho n’kosavuta kufalitsa matendawa.

“Ichi n’chifukwa china chomwe chimachititsa kuti m’nyengo yotentha matendawa afalikire kwambiri.

“Chinthu china chomwe chimachititsa izi n’choti m’nyengo yotentha nkhuku zimayenda mtunda wautali kusakasaka zakudya chifukwa chimachepa ndipo potero zimakatengako matendawa,” iye adatero.

Mphunzitsiyo adaonjeza kuti katemera wa chitopa sioopsa ndipo sasintha kaonekedwe ndi kakomedwe ka nyama ya nkhuku koma amangoiteteza basi.

Tanganyika adafotokoza kuti katemerayu sagwira ntchito ku nkhuku zomwe zagwidwa kale ndi matendawa choncho alimi akuyenera kutsatira ndondomeko.

“Katemerayu amagwira ntchito kwa miyezi inayi ndipo ichi n’chifukwa chake mlimi ayenera kupatsira m’miyezi inayi iliyonse,” iye adatero.

Tanganyika adaonjeza kuti zizindikiro za matendawa zimaonekera mbali ya thupi yomwe agwira.

Mwachitsanzo, iye adati akagwira mu ubongo khuku imapinda khosi, imazungulira malo amodzi kapena kumangogwa.

“Akagwira mapapo nkhuku imatsokomola, kuyetsemula ndi kutulutsa mamina. Akagwira m’matumbo nkhuku imatsegula m’mimba,” adafotokoza motero.

Share This Post