Chichewa

Ulimi wa mthirira n’chuma

Listen to this article

Tikudziweni…

Ndine Moffat Mtalimanja ndipo ndi mkazi wanga Effie timachokera m’mudzi wa Kaunde, ku Namadidi kwa Senior Chief Mlumbe m’boma la Zomba. Ndife alimi amene timaweta ziweto zosiyanasiyana kuphatikizaponso kuchita ulimi wa mbeu zosiyanasiyana. Pa ulimi wa mbeuzi timachita onse wa mvula komanso wa mthirira.

Ulimi wa mthirira mudauyamba liti?

Ulimiwu tidauyamba m’zaka za m’ma 1970 pamene bambo amagwira ntchito ku Portland Cement ku Changalume. Chimene chidatiyambitsa kuchita ulimiwu ndi kupewa kugula ndiwo za masamba omwe zimene timaona kuti tikhonza kuzikwanitsa kumazilimira ndi kumadzidyetsa tokha.

Mkati mwa njira ndi pamene tidaona kuti mbeu za masambazi ndi mpamba waukulu chifukwa anthu ozungulira kuno adayamba kumabwera kumatigula ndi pamene tidaonjezera moto kumachita ulimiwu mwakathithi.

Ndi mbewu ziti zimene mumalima?

Masambawo amafunika kuthirira

Tomato, kabichi, anyezi, beetroot, brocolli, nyemba, chimanga ndi mbeu zina zambiri malinga ndi kukonda kwa anthu ogula.

Kuchokera 1970 pali mtunda ndithu, chinsinsi chake chagona pati kuti muzilimabe mpaka pano?

Ulimi wa mthirira uli ndi chuma chobisika chimene alimi ambiri sanachitulukire. M’nyengo ya mvula, mbeu zambiri zikalimidwa ndipo zikakhwima pamsika zimakhala mbweee ndipo zimagulitsidwa pa mitengo yolira pamene m’nyengo yopanda mvula ndi mmene za masamba zimakhala zochepa koma ogula ndi ambiri. Apa mpamene mlimi wa nzeru amayenera kugwira mpini.

Ndi phindu lotani limene mumapeza mu ulimiwu?

Phindu limene timapeza mulimvetsetse ndi kuwerengera kuti anthu pakutha pa mwezi amagwiritsa ntchito ndalama zingati pogula tomato ndi masamba kuti azidya tsiku ndi tsiku pakhomo pawo. Mukhoza kuona kuti amagwiritsa ntchito ndalama zambiri zimene akanati masambawa alima okha ndiye kuti ndalama zimenezi akanapangira zinthu zina zofunika pakhomo pawo.

Pachifukwa chimenechi, sitigula chilichonse chokhudza masamba komanso timagulitsa masambawa kusonyeza kuti timapha mbalame ziwiri ndi ulimi wa nthilirawu. Pa chifukwa ichi ndalama zimene taziteteza posagula masambazo timapangira chitukuko chosiyanasiyana pakhomo pathu pano.

Ndi zovuta zotani zimene mukukumana nazo ndipo mumathana nazo motani?

Vuto lalikulu ndi madzi. Malo amene timalimawa tidayetsetsa kusaka madzi kuti tikumbe chitsime koma madzi sanapezeke. Kotero madzi adapezeka patali ndithu pamene tinakumba chitsimecho choncho tinalemba ntchito anthu amene amakatunga madzi pa chitsimepo ndikumazathira mu migolo imene timatungamo ndi kumathilira mbeuzi.

Pakadali pano tili ndi malingaliro opeza makina opepera madzi amene adzipopa madzi pachitsimepo ndikumabweretsa ku dimba kuno kuti ulimiwu ufike pa mponda chimera.

Ulimi wa mthirira uli ndi phindu?

Kwambiri. Mwachitsanzo, talima tomato mitengo 650. Ndipo mbeu yakeyi imabereka bwino chifukwa imatha kubereka tomato osachepera 50. Ndiye pa mitengo 650 mtengo uliwonse ubereke tomato osachepera 50 ndiye mwachitsanzo tomato m’modzi adzigulitsidwa K50 mukapanga masamu mukupeza bwa?

Komanso kabichi amene timalima ndi mbeu yaikulu bwino amene m’modzi timagulitsa K250 ndiye ngati tadzala oposa 100 mukhoza kuona kuti paphedwa makwacha ochuluka bwanji?

Chimanga chachiwisi nacho cha nthilira chikachita bwino chimasanduka chitsulo cha ndege pa msika, kotero ngati walima chochuluka mlimi satola chikwama?

Mbeu zina monga nyemba, tanaposi, beetroot, brocolli nazo ndi golide kale mchilengedwe chake kotero ngati mlimi akulima zimenezi mwakathithi umphawi ungakhale ndi ulamuliro pa moyo wake?

Ngati dziko titani kuti ulimi wa nthilira udzipindulira dzikoli?

Chofunika alimi asinthe kaganizidwe ndipo avomereze kuti ulimi wa nthilira ndi ulalo opititsa chuma chawo chomwe komanso cha dziko pa tsogolo. Zimatiwawa kumaona munda umene uli pafupi ndi msinje wakuti suphwera koma palibe chikulimidwapo kudikilira mvula basi uku kumakhala kuseweretsa ndalama.

Boma komanso mabungwe amene amalimbikitsa ulimi ayedzeke chidwi chawo powapatsa mphamvu alimi ndi zipangizo zimene zingatakasile ulimi wa nthilira kuti upite pa tsogolo chifukwa nthaka ndi madzi mdziko muno ndi zambiri. Ngati ife tikukwanitsa kuchita ulimi ndi madzi a pa chitsime tsono amene minda yawo ili pafupi ndi madziyo angapindule bwa?

Tilimbikitsenso achinyamata kuti pamene akusakasaka ntchito zamu ofesi aganizirenso zochita ulimi chifukwa ulimi ukhoza kusintha miyoyo yawo nkuthwanima kwa diso.

Ndi ubwino wotani umene ulipo ochita ulimi ngati banja?

Pamakhala kudalirana kwakulu, mwachitsanzo, ulimi umenewu amene amakhala patsogolo ndi mayi ndipo ine ndimangothandizira mapeto ake nzeru zawo ndi zanga tikaziphatikiza pamodzi ndi zimene zimachititsa kuti zinthu zizitiyendera bwino chotere. Muli mphamvu mukudalirana.

Related Articles

Back to top button
Translate »