Nkhani

Womuganizira kutaya khanda lake anjatidwa

Listen to this article

 

Anthu okhala m’dera la Hilltop m’mzinda wa Mzuzu adadzidzimuka Lamulungu lapitali, mayi wina wapabanja wochokera m’derali atadziwika kuti adataya mwana m’chimbudzi chokumba.

Malinga ndi anthu ozungulira nyumba ya Taona Chonga, wochokera m’mudzi mwa Mzukuchonga, m’boma la Mzimba, anthuwo adadabwa chimodzi mwa zimbudzi za pamalowa chikutulutsa fungo lodabwitsa.

Malo ake ndi awa: Mmodzi mwa anthu okhala ku Hilltop kusonyeza dzenje la chimbudzi chomwe mudatayidwa khandalo
Malo ake ndi awa: Mmodzi mwa anthu okhala ku Hilltop kusonyeza dzenje la chimbudzi chomwe mudatayidwa khandalo

“Fungoli linatidabwitsa ndipo pokumbukira kuti Chonga adali ndi pathupi pomwe panasowa, tinadziwitsa a mfumu kuti afufuze,” adatero mmodzi mwa anthuwo.

Iwo adati mphekesera zili ponseponse kuti mayiyo adakangana ndi mwamuna wake yemwe amachita bizinesi ya kabaza.

“Akuti mwamuna wake amati pathupipo si pake ndipo mkaziyo azipita kwa mwini pathupipo,” iwo adatero.

Mkazi wa mfumu Chikundura ya deralo adati amayi anayamba kumudabwa mnzawoyo ataona kuti pathupi pomwe adali napo pasowa koma alibe khanda.

“Titamuona kuti alibe pathupi tili kumadzi, tidadabwa ndi kumufunsa komwe wasiya khanda lake, koma iye adakanitsitsa kuti adalibe pathupi, kunali kunenepa chabe,” adatero mayi Chikundura.

Iye adati apo ndi pomwe adadziwitsa akuluakulu kuti mnzawoyo wataya khanda.

Ndipo nawo apolisi a mumzindawu atsimikiza kuti akusunga m’chitolokosi Chonga, wa  zaka 28, pomuganizira kuti adataya mwana m’chimbudzi.

Malinga ndi mneneri wa polisi ya Mzuzu, Martin Bwanali, Chonga, yemwe ali ndi ana asanu ndi mmodzi, komanso wina wakubere wa chaka ndi miyezi 7, adauza apolisi kuti adagwetsera chinthu m’chimbudzimo atapita kokadzithandiza.

Bwanali adati Chonga aonekera kubwalo la milandu masiku akubwerawa kukayankha mlandu wobisa pathupi.

Iye adati mayiyo adamutengera kuchipatala cha Mzuzu Central kuti akamuyeze ngatidi adali ndi pathupi koma zotsatira zidali zisadadziwike pomwe tinkasindikiza nkhaniyi.

Related Articles

Back to top button