Chichewa

Zotsamwitsa zachuluka

Listen to this article

Alimi omwe chipulumutso chawo cha chaka chino chili pa zipangizo zotsika mtengo m’pulogalamu ya Affordable Inputs Programme (AIP) alila mokweza ndi momwe pulogalamuyo ikuyendera.

Kafukufuku wa Tamvani wapeza kuti mavuto adzaoneni akutha chilinganizocho moti alimi ambiri sadagulebe zipangizo ngakhale mvula yagwa m’madera ena.

Polankhula ndi atolankhani Lachisanu sabata yapitayo, nduna ya zamalimidwe Lobin Lowe adati mwa alimi 4.2 miliyoni omwe akuyenera kupindula m’pulogalamuyo, 394 000 okha ndiwo adali atagula pofika tsikulo.

Tamvani atazungulira m’madera ena m’chigawo chapakati kuti aone momwe zikuyendera, adapeza makamu aanthu m’madepo ogulitsira zipangizozo ndipo padali litaniya la mavuto omwe akukumana nawo. Izi zidali chomodzimodzi kumwera ndi kumpoto.

Amalawi kudikirira feteleza pamsika wa Lumbadzi

“Chomwe tikudabwa kwambiri n’choti tikungoona feteleza ndi mbewu zikutuluka koma mizere ya anthu siyikutha kusonyeza kuti pali anthu ena monga mavenda omwe akugula mwamseri,” adatero Ackim Zakeyo padepo ina ya ku Mponela m’boma la Dowa.

Uyu adadandaula za ogula mwachinyengo, koma Elizabeth Banda wa ku Chileka m’boma la Lilongwe adati anthu ogulitsa zipangizozo sakupereka uphungu wolondola zomwe zikupangitsa kuti alimi ambiri azigula zipangizo zosakwanira.

“Pena mlimi akafika akumuuza kuti feteleza palibe pali mbewu yokha kapena mbewu palibe pali feteleza yekha ndiye pakusadziwa, mlimi akupezeka kuti wagula chomwe chilipocho polingalira kuti chotsalacho adzagulabe koma akabwera kachiwiri akuuzidwa kuti makina akusonyeza kuti iyeyo adagula kale,” adatero Banda.

Tamvani idayendera m’madera monga Chezi, Mpingu, Chileka ndi Lumbadzi m’boma la Lilongwe, Dowa Turn Off ndi Mponela m’boma la Dowa ndi Waliranji komanso Nkhwazi m’boma la Mchinji koma nkhani yake idali ya mavuto okhaokha.

Lipoti la bungwe la zamalimidwe la CisaNet lidafotokoza mwachindunji kuti pulogalamu ya AIP ili ndi zofooka zomwe zikupereka mpata wakatangale komanso chinyengo chogulitsa zipangizo zosakwanira mlingo wake m’dziko muno.

Pulogalamu ya AIP idapatsidwa ndalama zokwana K160 biliyoni ndipo CisaNet yati ngati unduna wa zamalimidwe siukonza msanga mavuto omwe apezekawo ndiye kuti ndalama zonsezi zilowa m’madzi osapindula kanthu.

“Ndalama zomwe zalowa m’pulogalamuyi ndi zambiri koma popanda kusamala, palibe phindu lomwe lipezeke ndipo zilowa m’madzi,” latero lipotilo.

Mwa zina, CisaNet yati unduna wa zamalimidwe sudakonze bwino ndondomeko yofalitsira uthenga okhudza pulogalamuyo moti akamberembere ambiri alemerera pamsana pa alimi chifukwa cha kusadziwa.

Potsimikiza kuti katangale ndi ukamberembere zakula m’pulogalamuyo, likulu la polisi lati anthu 19 amangidwa kale chifukwa chokhudzidwa ndi zachinyengo zosiyanasiyana.

Mneneri wapolisi James Kadadzera wati mwa anthu omwe akumveka kuti akuchita nawo za chinyengo ndi ogulitsa zipangizozo, mafumu, mavenda komanso apolisi ena omwe akuyang’anira ntchitoyi.

“Malipoti akubwera ochuluka koma anthu asade nkhawa chifukwa apolisi akufufuza malipoti onse ndipo takhazikitsa njira zina zochitira kalondolondo,” watero Kadadzera.

Kadaulo pa zamalimidwe Tamani Nkhono Mvula adati mavuto omwe ali m’pulogalamu ya AIP akufunika kukonzedwa mwachangu kuti ioneke phindu lake.

“Vuto ndi loti mavuto awawa akalekeleredwa chisanduka chizolowezi moti mtsogolo monsemo nkhani yake izikhala yomweyo mpaka sitidzaona cholowa pa mpamba onse omwe tikulowetsa mu AIP,” adatero iye.

Poyendera madepo ena ogulitsa zipangizozo kuchigwa cha Shire, nduna yofalitsa nkhani Gospel Kazako adatsindika kuti boma sililekelera zachinyengo zilizonse m’pulogalamuyo.

“Omwe akupanga kapena akukonzekera kupanga zachinyengo m’pulogalamuyo adziwe kuti akuzisanutsa adani a boma ndipo tithana nawo,” adatero Kazako.

Lowe adati unduna wake udakumana kale ndi oyang’anira za AIP m’madera onse m’dziko muno ndi kukambirana nawo za mavuto omwe atuluka m’pulogalamuyo.

Iye adati vuto lalikulu lomwe likukokera pulogalamuyo mmbuyo ndi la netiweki koma tsopano akadaulo akonza pomwe pamavuta ndipo alimi akugula popanda mavuto.

“Akapitawo onse aphunzitsidwa mokwanira zoyenera kuchita kuti mavutowa asaonekenso m’madera mwawo ndipo zonse zikhala bwino,” adatero Lowe.

Related Articles

Back to top button
Translate »