Chichewa

Achita phwando ndi kuimitsidwa kwa Kuluunda

Listen to this article

 

Lero kuli madyerero m’mudzi mwa Senior Chief Bibi Kuluunda m’boma la Salima kusangalalira kuti mfumuyi yaimitsidwa kugwira ntchito yake m’bomali.

Anthu a m’mudzimu kuphatikizaponso mafumu ena akhala akubindikira kuofesi ya DC wa bomali pofuna kukakamiza boma kuti ichotse mfumuyi poiganizira kuti ndi yaziphuphu.

Anthuwa adayamba mbindikirowo pa 11 April wapiyatu.

Lachitatu lapitali mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adasayina kalata yoimitsa Kuluunda amene wakhala paufumuwu kwa zaka 20, kupereka chimwemwe kwa anthuwa.

Mtsogoleri wa anthuwa, Muhammad Chingomanje, adati chimwemwe ndi chosayamba.

Wayamba waimitsidwa ufumu: Kuluunda
Wayamba waimitsidwa ufumu: Kuluunda

“Lero [Lachinayi pa 5 May] lidzakhala tsiku lachimwemwe pamoyo wanga. Lero lidzakhala tsiku lapaderadera m’mbiri ya dziko la Malawi, maka kwa ife anthu a ku Salima.

“Titagona panja pa ofesi ya DC kwa masiku 24, lero yankho labwera. Aliyense ndi wokondwa komanso wachimwemwe ndi zomwe zachitika lero,” adatero Chingomanje.

Kulankhula ndi Chingomanje pafoni kudali kovutirapo chifukwa cha nyimbo zomwe anthu amaimba komanso phokoso lachimwemwe lomwe limamveka.

Nyakwawa Chilaboto ya mwa Gulupu Kawanga m’dera la Kuluunda, idati iye komanso mafumu onse 31 amene amachita nawo mbindikirowo ndi okondwa ndi ganizo la Mutharika.

“Mtendere wadza m’mudzi mwanga limodzi ndi anthu anga 1 800 amene ndimawalamulira. Takhala tikulira ndi mfumuyi kwa zaka koma maso athu adali kuboma kuti atiyankhe. Lero ndi chimwemwe paliponse,” idatero mfumuyi uko akuimba nyimbo yachimwemwe.

Mfumuyi idati lero kukhala phwando chifukwa yankho labwera. “Tikupha ng’ombe komanso mbuzi, tikhala ndi tsiku lalikulu Lamulunguli chifukwa zomwe timapempha zayankhidwa.

“Aliyense abweretsa zakudya kusangalala kuti tsiku lomwe timaliyembekeza lakwana,” adatero Chilaboto.

Iye adati monga mfumu, nkhani ya kuimitsidwa kwa Kuluunda ithandiza ntchito yake chifukwa “kwa nthawi ndakhala ndikulimbana ndi amfumuwa pankhani zoti nanunso simungazimvetsetse. Nthawi yoti tipume yakwana tsopano”.

 

Titaimbira foni Kuluunda kuti timve maganizo ake, adangoti: “Ndili m’minibasi ndiye sitingamvane. Mundiimbirenso.”

Titaimbanso mfumuyi sidayankhe foni.

Malinga ndi nduna ya maboma aang’ono Kondwani Nankhumwa, Mutharika waganiza zoimitsa Kuluunda malinga ndi nkhani za katangale zomwe mfumuyi ikukhudzidwa nazo monga zoti idalandira K30 miliyoni ya Green Belt Initiative zoti igawire anthu okhudzidwa ndi polojekitiyi, koma sidalongosole komwe idapita K15 miliyoni.

Tsamba 22: 03 la gawo lachiwiri lokhudza malamulo a mafumu (Chiefs Act) limapereka mphamvu kwa mtsogoleri wa dziko kuti angathe kuchotsa mfumu ngati yachita zinthu mosemphana ndi udindo wake. n

Related Articles

Back to top button
Translate »