Akufuna boma likweze malipiro

Bungwe loona za ufulu wa anthu ogwira ntchito la Malawi Congress of Trade Union (MCTU) lapempha boma kuti likweze mlingo wa ndalama zotsikitsitsa zomwe munthu angalandire, komanso kuti anthu amene amalandira ndalama zochepera K50 000 pamwezi asamakhome  msonkho.

Polankhula pamwambo wokumbukira tsiku la ogwira ntchito Lolemba ku Lilongwe, mkulu wa bungwelo Luther Mambala adapempha boma kuti lionjezere ndalama za ogwira ntchito zotsikitsitsa zichoke pa K25 000 kufika pa K45 000. Ndipo adati okhoma msonkho azikhala olandira K50 000 kupita mtsogolo osati K25 000 monga zilili pano.

Mambala: Zinthu zakwera

Mambala adati akufunitsitsa boma litengere nkhaniyi ku Nyumba ya Malamulo kuti aphungu akaikaimbirane. Nyumba ya Malamulo imayembekezeka kutsegulidwa dzulo ndipo aphungu akambirana ndondomeko ya chuma.

“Chiyembekezo chathu n’choti nkhaniyi ifike kwa aphungu amene angatithandize,” adatero Mambala.

Bungweli lidapemphanso boma kuti lipeze njira zothetsera kuzimazima kwa magetsi zomwe ati zakhudza makampani kuti azipeza phindu lokwanira zomwe zikupangitsa kuti ena awachotse ntchito.

Mneneri wa boma Nicholas Dausi adalangiza bungwelo kuti lipereke madandaulo awo ku unduna wa zachuma omwe ungatengere nkhaniyi ku Nyumba ya Malamulo.

“Sindinganene zomwe boma lichite koma kungowalangiza kuti nkhaniyi aitengere ku unduna wa zachuma womwe ungatsatize bwino nkhaniyi,” adatero Dausi.

Share This Post