Chichewa

Amuganizira kupha apongozi ndi mpeni

Listen to this article

 

Madzi achita katondo m’mudzi mwa Chibwana kwa T/A Mankhambira, m’boma la Nkhata Bay komwe mayi wina wa zaka 27  akumuganizira kuti wabaya ndi kupha apongozi ake a zaka 64 ati kaamba koti adatengapo gawo pothetsa banja lake.

Mneneri wa apolisi m’bomali, Ignatious Esau, watsimikiza kuti apolisi atsekera m’chitokolosi Sylvia Chirwa ndi kumutsekulira mlandu womuganizira kupha Leah Banda mosemphana ndi ndime 209 ya malamulo a dziko lino.

Chirwa adaonekera bwalo la milandu la Nkhata Bay Lachitatu komwe mlandu wake adaupereka m’manja mwa bwalo la milandu lalikulu chifukwa mabwalo a majisitireti saweruza milandu yakupha.

Pakadalipano Chirwa ali palimandi kundende ya Nkhata Bay.

Esau wauza Msangulutso kuti Chirwa adagwidwa pomwe sing’anga yemwe adathamangirako pofuna mankhwala oti apulumuke ku mlanduwu adaulula.

Akumuganizira kuti adapha apongozi ake: Chirwa
Akumuganizira kuti adapha apongozi ake: Chirwa

“Malinga ndi kufufuza kwathu, Chirwa adalongosolera sing’angayu kuti wapha munthu ndipo amati akufuna mankhwala oti asakhale ndi mlandu. Sing’anga nkhaniyi idamukulira ndipo adauza anthu ena omwe adadziwitsa ife apolisi,” adalongosola Esau.

Iye adati apolisi adamukwidzinga nawo unyolo woganiziridwayu ndipo pakadalipano ali palimandi kundende ya Nkhata Bay komwe akudikira kuti azengedwe mlandu wopha munthu, womwe chilango chake ndi kunyongedwa kapena kukhala kundende moyo wako wonse ukapezeka wolakwa.

Polongosola momwe nkhani yonse idayendera, Esau adati mwana wina wa mayi adaphedwayo, Lloyd Nkhata, adauza apolisi kuti Chirwa adakwatiwa ndi mchimwene wake yemwe amakhala m’dziko la South Africa kwa zaka 9.

Iye adati awiriwa ali ndi mwana mmodzi wa zaka zisanu.

Esau adati kaamba ka mavuto ena awiriwa adasiyana ndipo Chirwa adabwerera kumudzi ndipo mmbuyo muno naye mwamuna wake wakaleyu adafunsa mayi ake kuti ampezere mkazi wina.

“Mayiwa adapezadi mkazi wina, zomwe sizidasangalatse Chirwa. Akuti chibwerereni kuchokera ku Joni, Chirwa wakhala akuopseza kuti athana nawo apongozi akewo chifukwa adatengapo gawo pothetsa banja lake,” adatero Esau.

Iye adati mauwa adapherezera usiku wa la Mulungu lapitali pomwe Chirwa adauyatsa ulendo wa kwa apongozi akewo ndi kuwabaya ali mtulo.

Adatsimikiza za kugwidwa kwa Chirwa: Esau
Adatsimikiza za kugwidwa kwa Chirwa: Esau

“Adawabaya pamimba, atatha apo adabayanso malo anayi cha kumsanaku ndipo Banda adamwalirira m’njira popita kuchipatala chachikulu cha Nkhata Bay, komwe nawo achipatala adatitsimikizira kuti adafa chifukwa chotaya magazi,” adalongosola motero mneneri wa apolisiyu.

Lachinayi m’sabatayi Msangulutso udacheza ndi mfumu yaikulu Mankhambira yomwe idaperekeza malemuyo kuchipatala.

“Ife tidali kunyanja usiku wa la Mulungu, pomwe tidamva kulira ndipo titathamangirako tidauzidwa kuti munthu wapha mayi Banda akugona kuchipinda,” idalongosola motero mfumuyo.

Chibwana adati mwana wa mayiyo ndiye adawapeza mpeni uli kumsanaku.

“Tidawatenga ndi kuthamangira nawo kuchipatala…” idalongosola mfumu Mankhambira, koma foni idadukira panjira ndipo kuyesayesa kuimbanso sadapezekenso.

Mtembo wa malemu Banda udalowa m’manda Lachitatu masana. n

Related Articles

Back to top button
Translate »