Chichewa

Bwanji wodwala chikuku amasamalidwira kutchire?

Listen to this article
Tsaka: Akachira amakhalandi mphamvu zotakata
Tsaka: Akachira amakhalandi mphamvu zotakata

Makono ano munthu wodwala chikuku amasamalidwa pakhomo kapena kuchipatala ndipo malangizo amene kale ankatsatidwa adalekeka. Kalelo, wodwala chikuku ankakabisidwa kunkhalango kuti asakumane ndi munthu wotentha thupi. Awiriwa akangokumana matenda akuti amakula msinkhu. Kuthengoko kumachitikanji? Nanga wotentha thupi amadana ndi wodwalayu bwanji? BOBBY KABANGO adali m’mudzi mwa Mphonde kwa Senior Chief Ngabu ku Chikhwawa  ndipo akucheza ndi Eni Tsaka motere:

 

Tidziwane wawa….

Dzina langa ndi Eni Tsaka, ndi dzina lomwe makolo adandipatsa ndithu, ena amaganiza ngati ndidadzipatsa ndekha. Ndine mlimi wa thonje komanso mapira ndi mchewere. Ndakhalitsa m’dziko la South Africa moti ndidadzakhazikika m’dziko muno mu 1974.

 

Komatu dzuwa kuno, mukumva bwanji?

Lero bolani, palibe dzuwa apa kusiyanitsa ndi masiku ena. Tinangozolowera, n’chifukwa munandipeza nditavula malaya. Kuno malaya sitikhalanawo chidwi chifukwa cha kutenthaku.

 

Tikumva kuti kuno miyambo yakalekale ikuchitikabe, n’zoona?

Pali choletsa kuti miyambo isachitike kodi? Mwina ndimve kwa inu ngati pali choletsa komanso chifukwa chomwe akuletsera.

 

Koma ikuchitika?

Kwambiri. N’chifukwa ndikuti pali choletsa? Ife tikutsata zomwe makolo ankachita komanso adatiuza kuti tizichita. Za miyambo ndi zikhulupiriro sitidzasiya.

 

Kukakamira zachikale bwanji?

Kodi zachikale zisiyike chifukwa mwapita kusukulu? Vuto lake mukapita kusukulu mukumaona ngati miyambo ya makolo njopanda ntchito. Kaamba ka izi tikuvulala. Iyi ndi miyambo komanso zikhulupiriro za makolo athu, sitingasiye ndipo sitidzasiya.

 

Tamva kuti wotentha thupi sakumana ndi wodwala chikuku, n’zoona?

Ndi zenizeni zomwe mwauzidwazo. Munthu wodwala chikuku ndi mdani ndi wotentha thupi ndipo sayenera akumane, ndi ngozi imeneyi.

 

Kutentha thupi n’kutani?

Kutentha thupi kutanthauza kuti wagonana ndi mwamuna kapena mkazi.

 

Zikachitika ndiye kuti watentha thupi?

Zimatero kumene. Thupi silimatentha popanda munthu wolitenthetsa, pamayenera pakhale wina amene amachititsa thupi lija kuti lichite juuu! Ndipo izi zimachitika ngati mwamuna kapena mkazi wachita motero.

 

Mawu amenewa akuchokera pati?

Akuchokera pantchito yomwe mwamuna ndi mkazi amachita, pajatu ntchito imeneyi imachititsa thupi kutentha. Mawuwatu akuchokera pamenepo.

 

Ndiye akatentha sayenera kukumana ndi wodwalayu?

Ndipo asakumane, ndi ngozi iyi. Kuno tikupangabe zimenezi.

 

Kukumana kwake kotani?

Tiyerekeze kuti m’nyumbamu mwagona wodwala, wotentha thupi asayandikirenso pakhomopo ndipo azingolambalala. Mphepo yokhayo ingathe kupha wodwalayu chifukwa mphepo yake imakhala yamoto.

 

Ndiye mumamusamala bwanji wodwalayu?

Mukadziwa kuti nthenda yafika timamutengera kuthengo loyandikana ndi nyumba yake komwe amakakhala mpaka atachira koma madzulo okha timamubweretsa.

 

Amakakhala ndi yani kuthengoko? Nanga imakhala nthawi yanji yomwe mumamubweretsa?

Kuthengoko kumakhala makolo ake ndi ena achibale, ochepa koma. Awa ndiwo amamusamala pomupatsa chakudya komanso kumumwetsa mankhwala achikukuwo. Usiku anthu atagona mpomwe timabwera naye kunyumba ndipo mbandakucha timamutengeranso kuthengoko.

 

Mumamupatsa mankhwala anji?

Timatenga makungwa a mtengo wa theza ndiye timawanyika. Pakapita kanthawi amafewa ndiye amananda. Zikafika pamenepa timamuika kukhutu ndi mmaso koma zonsezi zichitikire kuthengoko. Mukalondoloza zonse matendawo sachedwa kuchira.

 

Sizitheka kuti wodwalayu thupi lakenso ndi lotentha?

Aaaa! Inu munthu akudwala ndiye angakhalenso ndi nthawi kapena mphamvu zotenthetsa thupi? Sizingatheke koma akachira ndiye amakhala ndi mphamvu zotakata momwe angathere.

 

Koma amachira ndi zomwe mwanenazi?

Zimatheka, taona anthu akuchira koma akapanda kutsata mwambo ndi kumachita zinthu limodzi ndi wotentha thupi ndiye sipatha masiku mumva wamwalira.

 

Koma ndi mwambo wabwino?

Kwambiri ndipo sumamva kuti wina wamwalira chifukwa cha matenda amenewa koma vuto ndi chizungu. Talowetsa chizungu kwambiri n’chifukwa tikuyesa zikhulupiriro za makolo ngati zachabe.

Related Articles

Back to top button
Translate »