Chisamaliro choyenera cha ng’ombe za mkaka

Ngakhale alimi ambiri a ng’ombe za mkaka amabwekera kuti akupeza phindu ku ulimiwu, Jacob Mwasinga, mlangizi wa ziweto ku Mzuzu Agricultural Development Division (Mzadd) akuti alimi akhonza kusimba lokoma atasamalira moyenera ziweto zawo.

Malinga ndi mlangiziyu, ng’ombe ya mkaka ya mtundu wa Friesian yosasakaniza (pure breed) yomwe alimi ambiri akuweta, ili ndi kuthekera kotulutsa mkaka okwana malita 50 patsiku ngati ikudyetsedwa zakudya zoyenera ndi zokwanira, ikupatsidwa madzi nthawi zonse, ikukamidwa moyenera komanso ngati siikubisiridwa mwana pamene mlimi akukama.

Alimi ena akukama mkaka wochepa

Pamene izi zili chomwecho, alimi monga Taulo Chisoso ndi Chrissy Wyson a m’gulu la alimi lotchedwa Namahoya, kwa T/A Chimaliro, m’boma la Thyolo akuti akati apeza mkaka ochuluka, ndi okwana malitazi 15 okha pa ng’ombe imodzi ya mtunduwu.

“Madzi amathandizira kwambiri kuti ng’ombe ya mkaka itulutse mkaka wochuluka chifukwa pafupifupi 90 peresenti ya mkaka ndi madzi ndipo ichi n’chifukwa chake ng’ombe ya mkaka imatha kumwa madzi pafupifupi malita 200 patsiku.

“Ichi n’chifukwa chake m’khola la ng’ombezi m’mayenera kukhala madzi nthawi zonse. Chachiwiri, zakudya zoonjezera ku udzu womwe ng’ombezi zimadya monga gaga kapena zakasakaniza zija zimadziwika ndi dzina loti dairy marsh pachizungu, zimathandizira kuti ng’ombezi zitulutse mkaka wochuluka,” adatero Mwasinga.

Iye adati ng’ombe ya mkaka imayenera ikamidwe kawiri, masana ndi  madzulo ndipo pokama, mlimi awonetsetse kuti wachotsa mkaka wonse chifukwa izi zimathandiza kuti ng’ombe ipangenso mkaka wina.

Kuonjezera apo, iye adati ng’ombe zina zimakhala ndi chizolowezi chobisa mkaka ngati mwana wake sanayamweko kapena ngati mwana wake siyikumuona pafupi nthawi yomwe ikukamidwa choncho mwana amayenera akhale patsogolo kuti izitha kumuona komanso amayenera ayamweko pang’ono kenako kumuchotsa ndi kuyamba kukama.

Pothirirapo ndemanga pa nkhani ya kadyetsedwe, Jonathan Tanganyika, mphunzitsi wa ziweto ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) adati mlimi akhonzanso kumaonjezera chakudya monga gaga kapena chakasakaniza kufikira ataona kuti ng’ombe yafika pamalekezero opanga mkaka ochuluka, singathenso kupitiriza ngakhale ataonjezera chakudya china.

Iye adafotokoza kuti mlimi amayenera kudyetsera ng’ombe za mkaka chakudya chopangidwa kuchokera ku mbewu kawiri patsiku, sayileji kamodzi kapena kawiri patsiku makamaka mlimi akamaliza kukama pomwe heyi akuyenera kumapezeka nthawi zonse kuti zizidya umo zafunira ndipo poopetsa kuti udzu wina ukhonza kumangoonongeka, ndi bwino kuti mlimi aziyika pang’onopang’ono.

“Kadyetsedwe komanso mlingo wa chakudya sukuyenera kusintha kwa chaka chonse  chifukwa ukasintha, mkakanso umachepa. Chakudya cha ng’ombe za mkaka chotchipa  ndi udzu koma nthawi zambiri umachuluka nthawi ya dzinja kotero mlimi amayenera kufutsa mu njira ya heyi komanso sayilegi kuti apitirize  kudyetsera bwino ng’ombe zake kwa chaka chonse,” iye adatero.

Tanganyika adaonjeza kuti popanga heyi, mlimi akuyenera kusakanizako udzu wa mgulu la nyemba monga gilisidiya, zotsalira popanga shuga zotchedwa molasezi komanso mchere kuti adzakhale wa michere yochuluka ndi wokoma.

Ngakhale izi zili chomwechi, Tanganyika adati mlimi akuyeneranso kudziwa kuti ng’ombe ya mkaka ikabereka kokwana kasanu, imayamba kutulutsa mkaka ochepa komanso khola ngati lili losasamalirika, matenda monga yotupitsa bere (mastitis) amene amachepetsanso mkaka.

Iye adaonjezanso kuti mkaka umanka nuchulukira ng’ombe ikangoswa kumene kenako pakatha sabata 10, umayamba kuchepa mpaka kufika poumiratu. n

Share This Post