Nkhani

Chiyembekezo pa ntchito zakunja

Listen to this article
Ofuna ntchito ku Lilongwe ngati awa akufuna boma likonze zolakwika
Ofuna ntchito ku Lilongwe ngati awa akufuna boma likonze zolakwika

Pamene boma lalengeza kuti likulingalira zoyambanso kutumiza achinyamata kukagwira ntchito kumaiko ena, osowa ntchito ena ati ngakhale ndondomekoyi ndi yabwino, akukayika ndi momwe amasankhira okagwira ntchito kunjako.

Mneneri wa unduna wa za ntchito, Joyce Maganga, adati ntchito yotumiza achinyamata kunja imene idayamba muulamuliro wa Joyce Banda ipitirira. Iye adatsutsa kuti chipani cha DPP chidaimika ntchitoyi, imene achinyamata 100 000 amayenera kupeza mwayi wa ntchito ku South Korea, Quatar ndi Dubai.

“Chifukwa choti ntchitoyi idayamba ndi mtsogoleri wakale wa dziko lino, sizikutanthauza kuti ikuyenera kuimitsidwa kapena kutayidwa. Mtsogoleri wa dziko lino [Peter Mutharika] ali ndi ndondomeko zatsopano zopitirizira pologalamuyi,” adatero Maganga.

Malinga ndi nduna yakale ya achinyamata, Enoch Chihana, boma limafuna kuti achinyamata 2 000 atumizidwe kunja koma lidangokwanitsa kutumiza 800 okha, makamaka ku Dubai.

Achinyamata 15 000 adayesa mwayi wawo pachilinganizo choyamba koma adapeza mwayi sadapose 1 000.

Koma achinyamata ena, ati akukayika ngati osauka apindule pachilinganizochi.

Alfred Limbani wa zaka 29 ndipo amakhala ku Area 36 mumzinda wa Lilongwe adati adakondwera pomwe adamva kuti boma la Joyce Banda liyambitsa ndondomekoyi. Koma mvula ya masautso ake a ulova sidakate momwe amayembekezera.

“Ndidakondwa nditamva kuti kukudza mwayi wa ntchito. Koma sindidamve bwinobwino kuti opitawo amawasankha bwanji. Adatenga achinyamata.

“Zoti chilinganizochi chipitirira ndi nkhani yabwino koma tipemphe boma latsopanoli kuti libweretse poyera ndondomeko zotengera achinyamata ena ulendo uno komanso enafe tipindule nawo,” adatero Limbani.

Sibongile Manda, wa zaka 26, adati boma likuyeneranso kubwera poyera malinga ndi malipoti ena oti achinyamata ena amene adapeza mwayiwo amazunzika.

“Boma liyenera kukayendera kaye malo antchitowo kuti lionetsetse kuti achinyamata sakukumana ndi mavuto kumeneko. Komanso litenge ambiri kuti nafenso tipeze chochita,” adatero Manda.

Izi zidapherezera lipoti la Amnesty International limene mmbuyomu lidasonyeza kuti maiko monga South Korea ndi Qatar amazunza ogwira ntchito awo, makamaka amene akugwira ntchito zammunsi komanso ochokera kumaiko akunja.

Komatu chiyembekezochi sichili ndi achinyamata okha. Nawo akuluakulu monga Cydric Brazilo wa zaka 35, ali maso kunjira. Koma iye adati zachinyengo zimene zimachitika pandondomeko ya mmbuyomu zisakhaleko.

“Pologalamuyi tidaimva koma anthu timafooka nayo chifukwa choti kasankhidwe ka achinyamata okagwira ntchitoyi kamaoneka ngati kachinsinsi. Tikuona ngati adapita abale awo a akuluakulu a boma okha basi. Mnzanthu wina adapereka K15 000 n’kulembedwa dzina kuti apita koma adamuyenda pansi. Pano akadali lova kwawo ku Kasiya,” adatero iye.

Kulipira ndalama kotere, malinga ndi Patrick Bvumbwe wa zaka 44, nkusupula amphawi amene akufuna ntchito.

“Mmbuyomu zimamveka kuti wofuna ntchito apereke ndalama, tsono amphawife tizipeza kuti ndalamazo?” adatero iye.

Malinga ndi Maganga, ntchitoyi idakumana ndi mikwingwirima ku South Korea kokha. Ngakhale boma linkati lidagwirizana ndi boma la South Korea kuti litumizako achinyamata, mmodzi mwa akuluakulu oona za kunja kwa dzikolo Moon Sung Hwan adati padalibe mgwirizano ulionse pakati pa maboma awiriwo.

“Vuto tinali nalo ndi lokhudza dziko la South Korea. Kumeneku kokha ndiye ntchitoyi tidaimitsa kaye. Koma kumaiko a Dubai ndi Kuwait ikupitirira,” adatero mneneriyo.

Mlembi wamkulu wa ungano wa mabungwe oyang’anira apantchito wa Malawi Congress of Trade Union (MCTU), Elijah Kalichero, adati bungwelo lakhala likutsutsana ndi ndondomekoyi chifukwa achinyamata ambiri amakumana ndi zokhoma kumaiko achilendoko.

“Takhala tikulandira malipoti oti achinyamata ambiri amazunzidwa ndi kugwira ntchito zakalavulagaga kumaiko kumene amapitako. Komanso ambiri akugwira ntchito zosiyana ndi zimene adalonjezedwa. Ena akufunitsitsa atabwerera kuno kumudzi,” adatero Kalichero.

Tidalephera kulankhula ndi nduna ya zantchito Henry Mussa kuti timve ndondomeko zimene boma lakonza kuti mavuto amene adalipo mmbuyomu athe chifukwa samayankha foni yake.

Related Articles

Back to top button
Translate »